Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa

Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano


Masalimo 51 - Buku Lopatulika Buku Lopatulika
Masalimo 51

Davide avomereza kuchimwa kwake, apempha Mulungu amkhululukire, asamchotsere Mzimu Woyera
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide; m'mene anamdzera Natani mneneriyo atalowa iye kwa Bateseba.

1 Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zanu zokoma mufafanize machimo anga.

2 Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga, ndipo mundiyeretse kundichotsera choipa changa.

3 Chifukwa ndazindikira machimo anga; ndipo choipa changa chili pamaso panga chikhalire.

4 Pa Inu, Inu nokha, ndinachimwa, ndipo ndinachichita choipacho pamaso panu; kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu, mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu.

5 Onani, ndinabadwa m'mphulupulu, ndipo mai wanga anandilandira m'zoipa.

6 Onani, Inu mukondwera ndi zoonadi m'malo a m'katimo; ndipo m'malo a m'tseri mudzandidziwitsa nzeru.

7 Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbuu woposa matalala.

8 Mundimvetse chimwemwe ndi kusekera, kuti mafupawo munawathyola akondwere.

9 Muzibisire nkhope yanu zolakwa zanga, ndipo mufafanize mphulupulu zanga zonse.

10 Mundilengere mtima woyera, Mulungu; mukonze mzimu wokhazikika m'kati mwanga.

11 Musanditaye kundichotsa pamaso panu; musandichotsere Mzimu wanu Woyera.

12 Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu; ndipo mzimu wakulola undigwirizize.

13 Pomwepo ndidzalangiza ochimwa njira zanu; ndipo olakwa adzabwera kwa Inu.

14 Mundilanditse kumlandu wa mwazi, Mulungu, ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; lilime langa lidzakweza nyimbo ya chilungamo chanu.

15 Ambuye, tsegulani pa milomo yanga; ndipo pakamwa panga padzalalikira ulemekezo wanu.

16 Pakuti simukondwera ndi nsembe, mwenzi nditapereka; nsembe yopsereza simuikonda.

17 Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.

18 Chitirani Ziyoni chokoma monga mwa kukondwera kwanu; mumange malinga a miyala a Yerusalemu.

19 Pamenepo mudzakondwera nazo nsembe zachilungamo, ndi nsembe yopsereza ndi yopsereza yathunthu; pamenepo adzapereka ng'ombe paguwa lanu la nsembe.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi