Kupempherera mfumu potulukira iye kunkhondoKwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide. 1 Yehova akuvomereze tsiku la nsautso; dzina la Mulungu wa Yakobo likuike pamsanje; 2 likutumizire thandizo lotuluka m'malo oyera, ndipo likugwirizize kuchokera mu Ziyoni; 3 likumbukire zopereka zako zonse, lilandire nsembe yako yopsereza; 4 likupatse cha mtima wako, ndipo likwaniritse upo wako wonse. 5 Tidzafuula mokondwera mwa chipulumutso chanu, ndipo m'dzina la Mulungu wathu tidzakweza mbendera; Yehova akwaniritse mapempho ako onse. 6 Tsopano ndidziwa kuti Yehova apulumutsa wodzozedwa wake; adzamvomereza mu Mwamba mwake moyera ndi mphamvu ya chipulumutso cha dzanja lake lamanja. 7 Ena atama magaleta, ndi ena akavalo; koma ife tidzatchula dzina la Yehova Mulungu wathu. 8 Iwowa anagonjeka, nagwa; koma ife tauka, ndipo takhala chilili. 9 Yehova, pulumutsani, mfumuyo ativomereze tsiku lakuitana ife. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi