Okhulupirira onse alemekeze Mulungu wao1 Aleluya, Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano, ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake. 2 Akondwere Israele mwa Iye amene anamlenga; ana a Ziyoni asekere mwa mfumu yao. 3 Alemekeze dzina lake ndi kuthira mang'ombe; amuimbire zomlemekeza ndi lingaka ndi zeze. 4 Popeza Yehova akondwera nao anthu ake; adzakometsa ofatsa ndi chipulumutso. 5 Okondedwa ake atumphe mokondwera mu ulemu: Afuule mokondwera pamakama pao. 6 Nyimbo zakukweza Mulungu zikhale pakamwa pao, ndi lupanga lakuthwa konsekonse m'dzanja lao; 7 kubwezera chilango akunja, ndi kulanga mitundu ya anthu; 8 kumanga mafumu ao ndi maunyolo, ndi omveka ao ndi majerejede achitsulo, 9 kuwachitira chiweruzo cholembedwacho. Ulemu wa okondedwa ake onse ndi uwu. Aleluya. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi