Kudandaula kwa Ayuda ku Babiloni1 Ku mitsinje ya ku Babiloni, kumeneko tinakhala pansi, inde tinalira, pokumbukira Ziyoni. 2 Pa msondodzi uli m'mwemo tinapachika mazeze athu. 3 Popeza pamenepo akutigwirawo anatifunsa nyimbo ndipo akutizunza anafuna tisekere, ndi kuti, Mutiimbire nyimbo imodzi ya ku Ziyoni. 4 Tidati, Tidzaimba bwanji nyimbo ya Yehova m'dziko lachilendo? 5 Ndikakuiwalani, Yerusalemu, dzanja lamanja langa liiwale luso lake. 6 Lilime langa limamatike kunsaya zanga, ndikapanda kukumbukira inu; ndikapanda kusankha Yerusalemu koposa chimwemwe changa chopambana. 7 Yehova, kumbukirani ana a Edomu tsiku la Yerusalemu; amene adati, Gamulani, gamulani, kufikira maziko ake. 8 Mwana wamkazi wa ku Babiloni, iwe amene udzapasulidwa; wodala iye amene adzakubwezera chilango monga umo unatichitira ife. 9 Wodala iye amene adzagwira makanda ako, ndi kuwaphwanya pathanthwe. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi