Anthu onse alemekeze dzina la Mulungu wothandiza aumphawi1 Aleluya; Lemekezani, inu atumiki a Yehova; lemekezani dzina la Yehova. 2 Lodala dzina la Yehova Kuyambira tsopano kufikira kosatha. 3 Chitulukire dzuwa kufikira kulowa kwake lilemekezedwe dzina la Yehova. 4 Yehova akwezeka pamwamba pa amitundu onse, ulemerero wake pamwambamwamba. 5 Akunga Yehova Mulungu wathu ndani? Amene akhala pamwamba patali, 6 nadzichepetsa apenye zam'mwamba ndi za padziko lapansi. 7 Amene autsa wosauka kumchotsa kufumbi, nakweza waumphawi kumchotsa kudzala. 8 Kuti amkhalitse pamodzi ndi akulu, pamodzi ndi akulu a anthu ake. 9 Asungitsa nyumba mkazi wosaona mwana, akhale mai wokondwera ndi ana. Aleluya. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi