popeza mtima wako ngoolowa, ndipo unadzichepetsa pamaso pa Yehova muja udamva zonenera Ine malo ano ndi anthu okhalamo, kuti adzakhala abwinja, ndi temberero; ndipo unang'amba zovala zako ndi kulira misozi pamaso panga, Inenso ndakumvera, ati Yehova.
ndipo analowa, nakhalamo; koma sanamvere mau anu, sanayende m'chilamulo chanu; sanachite kanthu ka zonse zimene munawauza achite; chifukwa chake mwafikitsa pa iwo choipa chonsechi;
Chifukwa chake mkwiyo wanga ndi ukali wanga unathiridwa, nuyaka m'mizinda ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu; ndipo yapasudwa nikhala bwinja, monga lero lomwe.
Inde, anasanduliza mitima yao ikhale ngati mwala woti gwaa, kuti angamve chilamulo, ndi mau amene Yehova wa makamu anatumiza ndi Mzimu wake mwa aneneri oyamba aja; m'menemo munafuma mkwiyo waukulu wochokera kwa Yehova wa makamu.
Pakuti atero Yehova wa makamu: Monga ndinalingirira kuchitira inu choipa, muja makolo anu anautsa mkwiyo wanga, ati Yehova wa makamu, ndipo sindinawaleke;
Ndiye yani wa aneneri makolo anu sanamzunze? Ndipo anawapha iwo amene anaonetseratu za kudza kwake kwa Wolungamayo; wa Iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha;