Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 1:1 - Buku Lopatulika

1 Mwezi wachisanu ndi chitatu, chaka chachiwiri cha Dariusi, mau a Yehova anadza kwa Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido mneneri, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Mwezi wachisanu ndi chitatu, chaka chachiwiri cha Dariusi, mau a Yehova anadza kwa Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido mneneri, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Mwezi wachisanu ndi chitatu, chaka chachiŵiri cha ufumu wa Dariusi, Chauta adapatsa mneneri Zekariya, mwana wa Berekiya, mdzukulu wa Ido, uthenga uwu wakuti,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mwezi wachisanu ndi chitatu, mʼchaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo, Yehova anayankhula ndi mneneri Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido, kuti:

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 1:1
17 Mawu Ofanana  

Momwemo inalekeka ntchito ya nyumba ya Mulungu yokhala ku Yerusalemu; nilekeka mpaka chaka chachiwiri cha ufumu wa Dariusi mfumu ya Persiya.


Ndipo aneneri, Hagai mneneriyo, ndi Zekariya mwana wa Ido, ananenera kwa Ayuda okhala mu Yuda ndi mu Yerusalemu; m'dzina la Mulungu wa Israele ananenera kwa iwo.


wa Ido, Zekariya; wa Ginetoni, Mesulamu;


Ido, Ginetoyi, Abiya,


Chaka chachiwiri cha mfumu Dariusi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri kwa Zerubabele mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kuti,


tsiku la makumi awiri ndi anai la mwezi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, chaka chachiwiri cha mfumu Dariusi.


Pamenepo mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti,


Tsiku la makumi awiri ndi anai la mwezi wachisanu ndi chinai, chaka chachiwiri cha Dariusi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti,


Ndipo mau a Yehova anadza nthawi yachiwiri kwa Hagai tsiku la makumi awiri la mwezi, ndi kuti,


Tsiku la makumi awiri ndi chinai la mwezi wakhumi ndi chimodzi, ndiwo mwezi wa Sebati, chaka chachiwiri cha Dariusi, mau a Yehova anadza kwa Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido mneneri, ndi kuti,


Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, ndi kuti,


Ndipo kunachitika chaka chachinai cha mfumu Dariusi, mau a Yehova anadza kwa Zekariya tsiku lachinai la mwezi wachisanu ndi chinai, ndiwo Kisilevi.


kotero kuti udzafika pa inu mwazi wonse wotayidwa padziko lapansi, kuyambira kumwazi wa Abele wolungamayo, kufikira kumwazi wa Zekariya mwana wa Barakiya, amene munamupha pakati pa Kachisi ndi guwa la nsembe.


kuyambira mwazi wa Abele kufikira mwazi wa Zekariya, amene anamphera pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya Kachisi. Indetu, ndinena kwa inu udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uno.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa