Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Yohane 8:9 - Buku Lopatulika

Koma iwo, m'mene anatulukamo amodziamodzi, kuyambira akulu, kufikira otsiriza; ndipo Yesu anatsala yekha, ndi mkazi, alikuima pakati.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma iwo, m'mene anatulukamo amodziamodzi, kuyambira akulu, kufikira otsiriza; ndipo Yesu anatsala yekha, ndi mkazi, alikuima pakati.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma iwo atamva zimenezi, adayamba kuchokapo mmodzimmodzi, kuyambira akuluakulu; Yesu nkutsalira yekha, mai uja ali chikhalire pakati pompaja.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iwo atamva izi anayamba kuchoka mmodzimmodzi, akuluakulu poyamba, mpaka Yesu anatsala yekha ndi mkaziyo atayimirira pomwepo.

Onani mutuwo



Yohane 8:9
22 Mawu Ofanana  

Ndipo mkaziyo ananena ndi Eliya, Ndili nawe chiyani munthu iwe wa Mulungu? Kodi wadza kwa ine kundikumbutsa tchimo langa, ndi kundiphera mwana wanga?


Tsono mfumu inanenanso ndi Simei, Udziwa iwe choipa chonse mtima wako umadziwacho, chimene udachitira Davide atate wanga; chifukwa chake Yehova adzakubwezera choipa chako pamutu pako mwini.


M'mwamba mudzavumbulutsa mphulupulu yake, ndi dziko lapansi lidzamuukira.


kuti kufuula kokondwera kwa woipa sikukhalira kutha, ndi chimwemwe cha wonyoza Mulungu chikhala kamphindi?


Achite manyazi nadodome iwo akulondola moyo wanga kuti auononge. Abwerere m'mbuyo, nachite manyazi iwo okondwera kundichitira choipa.


Izi unazichita iwe, ndipo ndinakhala chete Ine; unayesa kuti ndifanana nawe, ndidzakudzudzula, ndi kuchilongosola pamaso pako.


Adani a moyo wanga achite manyazi, nathawe; chotonza ndi chimpepulo zikute ondifunira choipa.


pakuti kawirikawiritu mtima wako udziwa kuti nawenso unatemberera ena.


Ndipo pamene Iye anatero, onse aja akutsutsana naye ananyazitsidwa; ndipo anthu onse a m'khamu anakondwera ndi zinthu zonse za ulemererozo zinachitidwa ndi Iye.


Koma Yesu pamene adaweramuka, anati kwa iye, Mkazi iwe, ali kuti ajawa? Palibe munthu anakutsutsa kodi?


Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.


Koma mamawa anadzanso ku Kachisi, ndipo anthu onse anadza kwa Iye; ndipo m'mene anakhala pansi anawaphunzitsa.


Koma alembi ndi Afarisi anabwera naye kwa Iye mkazi wogwidwa m'chigololo, ndipo pamene anamuimika iye pakati,


Ndipo m'mene adaweramanso analemba ndi chala chake pansi.


popeza iwo aonetsa ntchito ya lamulolo yolembedwa m'mitima yao, ndipo chikumbumtima chao chichitiranso umboni pamodzi nao, ndipo maganizo ao wina ndi mnzake anenezana kapena akanirana;


Iwe wakunena kuti munthu asachite chigololo, kodi umachita chigololo mwini wekha? Iwe wakudana nao mafano, umafunkha za mu Kachisi kodi?


m'mene monse mtima wathu utitsutsa; chifukwa Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.