Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 40:14 - Buku Lopatulika

14 Achite manyazi nadodome iwo akulondola moyo wanga kuti auononge. Abwerere m'mbuyo, nachite manyazi iwo okondwera kundichitira choipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Achite manyazi nadodome iwo akulondola moyo wanga kuti auononge. Abwerere m'mbuyo, nachite manyazi iwo okondwera kundichitira choipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Anthu ofunafuna moyo wanga, muŵachititse manyazi ndi kuŵasokoneza. Okhumba kundipweteka, abwezedwe m'mbuyo ndi kunyozedwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Onse amene akufunafuna kuchotsa moyo wanga achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa; onse amene amakhumba chiwonongeko changa abwezedwe mwamanyazi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 40:14
16 Mawu Ofanana  

Ichi chikhale mphotho ya otsutsana nane yowapatsa Yehova, ndi ya iwo akunenera choipa moyo wanga.


Ng'ombe zamphongo zambiri zandizinga; mphongo zolimba za ku Basani zandizungulira.


Landitsani moyo wanga kulupanga; wokondedwa wanga kumphamvu ya galu,


Achite manyazi, nadodome iwo akukondwera chifukwa cha choipa chidandigwera. Avekeke ndi manyazi ndi kupunzika iwo akudzikuza pa ine.


Athe nzeru nachite manyazi iwo akufuna moyo wanga; abwezedwe m'mbuyo nasokonezeke iwo akundipangira chiwembu.


Fulumirani kundipulumutsa, Mulungu! Fulumirani kundithandiza, Yehova.


Adani a moyo wanga achite manyazi, nathawe; chotonza ndi chimpepulo zikute ondifunira choipa.


Pobwerera m'mbuyo adani anga, akhumudwa naonongeka pankhope panu.


Taona, onse amene akukwiyira iwe adzakhala ndi manyazi, nasokonezedwa; iwo amene akangana ndi iwe adzakhala ngati chabe, nadzaonongeka.


Koma mwa Yehova yekha, wina adzati kwa Ine, muli chilungamo ndi mphamvu; ngakhale kwa Iyeyo anthu adzafika, ndi onse amene anamkwiyira, adzakhala ndi manyazi.


Ndipo m'mene anati kwa iwo, Ndine, anabwerera m'mbuyo, nagwa pansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa