Ndipo pamene dziko lonse la Ejipito linali ndi njala, anthu anafuulira Farao awapatse chakudya; ndipo Farao anati kwa Aejipito onse, Pitani kwa Yosefe: chimene iye anena kwa inu chitani.
Yohane 2:5 - Buku Lopatulika Amake ananena kwa atumiki, Chimene chilichonse akanena kwa inu, chitani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Amake ananena kwa atumiki, Chimene chilichonse akanena kwa inu, chitani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo amai ake adauza anyamata amene ankatumikira kuti, “Chilichonse chimene akuuzeni, muchite.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amayi ake anati kwa antchito, “Inu muchite chilichonse chimene akuwuzeni.” |
Ndipo pamene dziko lonse la Ejipito linali ndi njala, anthu anafuulira Farao awapatse chakudya; ndipo Farao anati kwa Aejipito onse, Pitani kwa Yosefe: chimene iye anena kwa inu chitani.
Ndipo ndinachita monga momwe anandilamulira, ndinatulutsa akatundu anga usana, ngati a pa ulendo wa kundende, ndi madzulo ndinaboola pakhoma ndi dzanja langa, ndinawatulutsa pali mdima, ndi kuwasenza paphewa panga pamaso pao.
Pamene Iye anali chilankhulire ndi makamu, onani, amake ndi abale ake anaima panja, nafuna kulankhula naye.
Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka kumalo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo anatuluka wosadziwa kumene akamukako.
ndipo pamene anakonzeka wamphumphu anakhala kwa onse akumvera Iye chifukwa cha chipulumutso chosatha;
Chilichonse chichokera kumpesa asadyeko, asamwe vinyo kapena choledzeretsa, kapena kudya chilichonse chodetsa; zonse ndinamlamulira azisunge.