Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 9:6 - Buku Lopatulika

6 komatu, uka, nulowe m'mzinda, ndipo kudzanenedwa kwa iwe chimene uyenera kuchita.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 komatu, uka, nulowe m'mudzi, ndipo kudzanenedwa kwa iwe chimene uyenera kuchita.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Koma dzuka, kaloŵe mumzindamo, ndipo akakuuza chochita.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 “Tsopano dzuka, lowa mu mzindamo, ndipo udzawuzidwa zoyenera kuchita.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 9:6
33 Mawu Ofanana  

Munthuyo wakuopa Yehova ndani? Adzamlangiza iye njira adzasankheyo.


Wodala munthu amene mumlanga, Yehova; ndi kumphunzitsa m'chilamulo chanu;


Ndaona njira zake, ndipo ndidzamchiritsa; ndidzamtsogoleranso, ndi kumbwezera iye ndi olira maliro ake zotonthoza mtima.


Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang'anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga.


Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, khala chilili, ndipo ndidzanena nawe.


Ndipo dzanja la Yehova linandikhalira komweko, nati kwa ine, Nyamuka, tuluka kunka kuchidikha, ndipo pomwepo ndidzalankhula ndi iwe.


Ndinamva, ndi m'mimba mwanga munabwadamuka, milomo yanga inanthunthumira pamau, m'mafupa mwanga mudalowa chivundi, ndipo ndinanjenjemera m'malo mwanga; kuti ndipumule tsiku lamsauko, pamene akwerera anthu kuti ayambane nao ndi makamu.


Koma ambiri oyamba adzakhala akuthungo, ndi akuthungo adzakhala oyamba.


Ndipo anthu a makamu anamfunsa iye, nanena, Ndipo tsono tizichita chiyani?


Ndipo anati, Kornelio kenturiyoyo, munthu wolungama ndi wakuopa Mulungu, amene mtundu wonse wa Ayuda umchitira umboni, anachenjezedwa ndi mngelo woyera kuti atumize nakuitaneni mumuke kunyumba yake, ndi kumvetsa mau anu.


Chifukwa chake tumiza anthu ku Yopa, akaitane Simoni amene anenedwanso Petro; amene acherezedwa m'nyumba ya Simoni wofufuta zikopa, m'mbali mwa nyanja.


acherezedwa iye ndi wina Simoni wofufuta zikopa, nyumba yake ili m'mbali mwa nyanja.


Koma pamene anamva ichi, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzachita chiyani, amuna inu, abale?


Ndipo ndinati, Ndidzachita chiyani, Ambuye? Ndipo Ambuye anati kwa ine, Tauka, pita ku Damasiko; kumeneko adzakufotokozera zonse zoikika kwa iwe uzichite.


Komatu uka, imirira pa mapazi ako; pakuti chifukwa cha ichi ndinaonekera kwa iwe, kukuika iwe ukhale mtumiki ndi mboni ya izi wandionamo Ine, ndiponso ya izi ndidzakuonekeramo iwe;


Koma anati, Ndinu yani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda;


Ndipo Yesaya alimbika mtima ndithu, nati, Ndinapezedwa ndi iwo amene sanandifune; ndinaonekera kwa iwo amene sanandifunse.


Pakuti pakusadziwa chilungamo cha Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa chilungamo cha iwo okha, iwo sanagonje ku chilungamo cha Mulungu.


Ndipo lamulo linalowa moonjezera, kuti kulakwa kukachuluke; koma pamene uchimo unachuluka, pomwepo chisomo chinachuluka koposa;


Ndipo kale ine ndinali wamoyo popanda lamulo; koma pamene lamulo linadza, uchimo unatsitsimuka, ndipo ine ndinafa.


Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira;


Koma apatsa chisomo choposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.


Ndipo uitane Yese abwere kunsembeko, ndipo Ine ndidzakusonyeza chimene uyenera kuchita; ndipo udzandidzozera iye amene ndidzakutchulira dzina lake.


Ndipo pamene Saulo anaona khamu la Afilisti, anaopa, ndi mtima wake unanjenjemera kwakukulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa