Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 41:55 - Buku Lopatulika

55 Ndipo pamene dziko lonse la Ejipito linali ndi njala, anthu anafuulira Farao awapatse chakudya; ndipo Farao anati kwa Aejipito onse, Pitani kwa Yosefe: chimene iye anena kwa inu chitani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

55 Ndipo pamene dziko lonse la Ejipito linali ndi njala, anthu anafuulira Farao awapatse chakudya; ndipo Farao anati kwa Aejipito onse, Pitani kwa Yosefe: chimene iye anena kwa inu chitani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

55 Njalayo itakwanira dziko lonse la Ejipito, anthu ankalirira Farao kuti aŵapatse chakudya. Farao ankaŵauza onse kuti, “Pitani kwa Yosefe, zimene akakulamuleni, mukachite zimenezo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

55 Pamene njala ija inakwanira dziko lonse la Igupto anthu analilira Farao kuti awapatse chakudya. Koma Farao anawawuza kuti, “Pitani kwa Yosefe ndipo mukachite zimene akakuwuzeni.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 41:55
13 Mawu Ofanana  

Ndipo njala inali padziko lonse lapansi; ndipo Yosefe anatsegula nkhokwe zonse nagulitsa Aejipito: ndipo njala inakula m'dziko la Ejipito.


Ndipo Yosefe anali wolamulira dziko; ndiye amene anagulitsa kwa anthu onse a m'dziko; ndipo anafika abale ake a Yosefe, namweramira pansi, nkhope zao pansi.


Akali chilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphimba iwo: ndipo onani, mau ali kunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.


ndipo onani, mau akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.


Amake ananena kwa atumiki, Chimene chilichonse akanena kwa inu, chitani.


Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.


Pakuti kunamkomera Atate kuti mwa Iye chidzalo chonse chikhalire,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa