Yohane 16:4 - Buku Lopatulika Koma zinthu izi ndalankhula ndi inu kuti ikadza nthawi yao, mukakumbukire kuti ndinakuuzani. Koma izi sindinanene kwa inu kuyambira pachiyambi, chifukwa ndinali pamodzi ndi inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma zinthu izi ndalankhula ndi inu kuti ikadza nthawi yao, mukakumbukire kuti ndinakuuzani. Koma izi sindinanena kwa inu kuyambira pachiyambi, chifukwa ndinali pamodzi ndi inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ndimati muzimve zimenezi kuti nthaŵi yakeyo ikadzafika, mudzakumbukire kuti ndidaakuuziranitu.” “Sindidakuuzeni zimenezi poyamba paja ai, chifukwa ndinali nanu pamodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndakuwuzani izi kuti nthawi ikadzafika mudzakumbukire kuti Ine ndinakuchenjezani kale. Ine sindinakuwuzeni izi poyamba paja chifukwa ndinali nanu.” |
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nao? Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya.
Ndipo Yesu ananena nao, Kodi akhoza kusala kudya anyamata a ukwati pamene mkwati ali pamodzi nao? Pokhala ali naye mkwati pamodzi ndi iwo sangathe kusala.
Kuyambira tsopano ndinena kwa inu, chisadachitike, kuti pamene chitachitika, mukakhulupirire kuti ndine amene.
pakuti Ine ndidzamuonetsa iye zinthu zambiri ayenera iye kuzimva kuwawa chifukwa cha dzina langa.
podziwa kuti kuleka kwa msasa wanga kuli pafupi, monganso Ambuye wathu Yesu Khristu anandilangiza.