Wodala Yehova Mulungu wa makolo athu, amene anaika chinthu chotere mu mtima wa mfumu, kukometsera nyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu,
Yohane 13:2 - Buku Lopatulika Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adatha kuika mu mtima wake wa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote, kuti akampereke Iye, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adatha kuika mu mtima wake wa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote, kuti akampereke Iye, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yesu ndi ophunzira ake ankadya chakudya chamadzulo. Satana nkuti ataika kale mumtima mwa Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote, maganizo akuti akapereke Yesu kwa adani ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atayamba kudya mgonero, mdierekezi anali atalowa kale mu mtima wa Yudasi Isikarioti mwana wa Simoni, kuti amupereke Yesu. |
Wodala Yehova Mulungu wa makolo athu, amene anaika chinthu chotere mu mtima wa mfumu, kukometsera nyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu,
Ndipo ndinauka usiku, ine ndi amuna owerengeka nane, osauza munthu yense ine choika Mulungu wanga m'mtima mwanga ndichitire Yerusalemu; panalibenso nyama ina nane, koma nyama imene ndinakhalapo.
Ndipo Satana analowa mwa Yudasi wonenedwa Iskariote, amene anawerengedwa mmodzi wa khumi ndi awiriwo.
ananyamuka pamgonero, navula malaya ake; ndipo m'mene adatenga chopukutira, anadzimanga m'chuuno.
Koma Petro anati, Ananiya, Satana anadzaza mtima wako chifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wake wa mundawo?
amene ife tonsenso tinagonera pakati pao kale, m'zilakolako za thupi lathu, ndi kuchita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo chibadwire, monganso otsalawo;
Pakuti Mulungu anapatsa kumtima kwao kuchita za m'mtima mwake, ndi kuchita cha mtima umodzi ndi kupatsa ufumu wao kwa chilombo, kufikira akwaniridwa mau a Mulungu.