Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 2:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo ndinauka usiku, ine ndi amuna owerengeka nane, osauza munthu yense ine choika Mulungu wanga m'mtima mwanga ndichitire Yerusalemu; panalibenso nyama ina nane, koma nyama imene ndinakhalapo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo ndinauka usiku, ine ndi amuna owerengeka nane, osauza munthu yense ine choika Mulungu wanga m'mtima mwanga ndichitire Yerusalemu; panalibenso nyama ina nane, koma nyama imene ndinakhalapo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Sindidauze ndi mmodzi yemwe zimene Mulungu wanga adaaika mumtima mwanga, zoti ndichitire Yerusalemu. Tsono ndidadzuka usiku pamodzi ndi anthu ena oŵerengeka. Ndinalibe bulu wina kupatula yekhayo amene ndidaakwerapo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Sindinawuze munthu aliyense za zimene Yehova anayika mu mtima mwanga kuti ndichitire mzinda wa Yerusalemu. Choncho ndinanyamuka usiku pamodzi ndi anthu ena owerengeka. Ndinalibe bulu wina aliyense kupatula amene ndinakwerapo.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 2:12
20 Mawu Ofanana  

Wodala Yehova Mulungu wa makolo athu, amene anaika chinthu chotere mu mtima wa mfumu, kukometsera nyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu,


Motero ndinafika ku Yerusalemu, ndi kukhalako masiku atatu.


Ndipo ndinatuluka usiku pa Chipata cha ku Chigwa, kunka kuchitsime cha chinjoka, ndi ku Chipata cha Kudzala, ndi kuyang'ana malinga a Yerusalemu adapasukawo, ndi zipata zake zothedwa ndi moto.


Mupempherere mtendere wa Yerusalemu; akukonda inu adzaona phindu.


Chitirani Ziyoni chokoma monga mwa kukondwera kwanu; mumange malinga a miyala a Yerusalemu.


Munthu wanzeru abisa zomwe adziwa; koma mtima wa opusa ulalikira utsiru.


mphindi yakung'amba ndi mphindi yakusoka; mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula;


Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israele atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika chilamulo changa m'kati mwao, ndipo m'mtima mwao ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, nadzakhala iwo anthu anga;


ndipo ndidzapangana nao pangano lamuyaya, kuti sindidzawachokera kuleka kuwachitira zabwino; koma ndidzalonga kuopsa kwanga m'mitima yao, kuti asandichokere.


Chifukwa chake wochenjerayo akhala chete nthawi yomweyo; pakuti ndiyo nthawi yoipa.


Musakhulupirira bwenzi, musatama bwenzi loyanja; usamtsegulire pakhomo pakamwa pako, ngakhale kwa iye wogona m'fukato mwako.


Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.


Ndipo iye ananyamuka natenga kamwana ndi amake usiku, nachoka kupita ku Ejipito;


Koma ayamikike Mulungu, wakupatsa khama lomweli la kwa inu mu mtima wa Tito.


Ndipo Yoswa anawadzidzimukitsa; popeza anakwera kuchokera ku Giligala usiku wonse.


Pakuti Mulungu anapatsa kumtima kwao kuchita za m'mtima mwake, ndi kuchita cha mtima umodzi ndi kupatsa ufumu wao kwa chilombo, kufikira akwaniridwa mau a Mulungu.


Pamenepo Gideoni anatenga amuna khumi mwa anyamata ake, nachita monga Yehova adanena naye; ndipo kunali, popeza anaopa akunyumba ya atate wake, ndi amuna akumudziwo, sanachichite msana, koma usiku.


Ndipo tsopano, taukani usiku, inu ndi anthu okhala nanu ndi kulalira kuthengo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa