Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 2:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo ndinatuluka usiku pa Chipata cha ku Chigwa, kunka kuchitsime cha chinjoka, ndi ku Chipata cha Kudzala, ndi kuyang'ana malinga a Yerusalemu adapasukawo, ndi zipata zake zothedwa ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo ndinatuluka usiku pa Chipata cha ku Chigwa, kunka kuchitsime cha chinjoka, ndi ku Chipata cha Kudzala, ndi kuyang'ana malinga a Yerusalemu adapasukawo, ndi zipata zake zothedwa ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Ndidatuluka usiku podzera ku Chipata cha ku Chigwa, nkuyenda cha ku Chitsime cha Chilombo Cham'madzi ndi ku Chipata cha Zinyalala. Ndipo ndidayang'ana makoma a Yerusalemu amene adaagamukagamuka ndiponso zipata zake zimene zidaaonongeka ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ndinatuluka usiku podzera ku Chipata cha ku Chigwa ndi kuyenda kupita ku Chitsime cha Chirombo Chamʼmadzi mpaka ku Chipata cha Zinyalala. Ndinayangʼana makoma a Yerusalemu, amene anagwetsedwa, ndi zipata zake, zimene zinawonongedwa ndi moto.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 2:13
9 Mawu Ofanana  

Uziya anamanganso nsanja mu Yerusalemu pa Chipata cha Kungodya, ndi pa Chipata cha ku Chigwa, ndi popindika linga; nazilimbikitsa.


Nanena nane iwo, Otsalawo otsala andende uko kudzikoko akulukutika kwakukulu, nanyozedwa; ndi linga la Yerusalemu lapasuka, ndi zipata zake zatenthedwa ndi moto.


Pamenepo ndinakwera nao akulu a Yuda pa lingali, ndinaikanso oyamikira magulu awiri akulu oyenda molongosoka; lina loyenda ku dzanja lamanja palinga kunka ku Chipata cha Kudzala;


Ndipo ndinauka usiku, ine ndi amuna owerengeka nane, osauza munthu yense ine choika Mulungu wanga m'mtima mwanga ndichitire Yerusalemu; panalibenso nyama ina nane, koma nyama imene ndinakhalapo.


Ndipo ndinakwera usiku kumtsinje, ndi kuyang'ana lingali; ndinabwerera tsono ndi kulowa pa Chipata cha ku Chigwa, momwemo ndinabwereranso.


Pamenepo ndinanena nao, Muona choipa m'mene tilimo, kuti Yerusalemu ali bwinja, ndi zipata zake zotentha ndi moto; tiyeni timange linga la Yerusalemu, tisakhalenso chotonzedwa.


Ndipo ndinati kwa mfumu, Mfumu ikhale ndi moyo kosatha; ilekerenji nkhope yanga kuchita chisoni, popeza pali bwinja kumzinda kuli manda a makolo anga, ndi zipata zake zopsereza ndi moto.


Kwerani pa makoma ake nimupasule; koma musatsirize konse; chotsani nthambi zake pakuti sizili za Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa