Ndipo mfumu ya Asiriya anatuma nduna ndi mkulu wa adindo ndi kazembe ochokera ku Lakisi ndi khamu lalikulu la nkhondo kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Nakwera iwo, nafika ku Yerusalemu. Ndipo atakwera, anafika, naima kumcherenje wa thamanda la kumtunda, ndilo la ku mseu wa ku Malo a Wotsuka Thonje.
Machitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi mphamvu yake yonse, ndi umo anamangira dziwe ndi mchera, nautengera mzinda madzi, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda?
Hezekiya yemweyo anatseka kasupe wa kumtunda wa madzi a Gihoni, nawapambutsa atsikire kumadzulo kwa mzinda wa Davide. Ndipo Hezekiya analemerera nazo ntchito zake zonse.
ndi ku Chipata cha ku Chitsime, ndi kundunji kwao, anakwerera pa makwerero a mzinda wa Davide, potundumuka linga, popitirira pa nyumba ya Davide, mpaka ku Chipata cha Madzi kum'mawa.
Ndi Chipata cha ku Kasupe anachikonza Salumu mwana wa Kolihoze mkulu wa dziko la Mizipa anachimanga, nachikomaniza pamwamba pake, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake; ndiponso linga la dziwe la Sela pamunda wa mfumu, ndi kufikira kumakwerero otsikira kumzinda wa Davide.
Potsatizana naye anakonza Nehemiya mwana wa Azibuki, mkulu wa dera lake lina la dziko la Betezuri, mpaka malo a pandunji pa manda a Davide, ndi ku dziwe adalikumba, ndi kunyumba ya amphamvu aja.