Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 22:31 - Buku Lopatulika

31 Simoni, Simoni, taona, Satana anafunsa akutengeni kuti akupeteni ngati tirigu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Simoni, Simoni, taona, Satana anafunsa akutengeni kuti akupeteni ngati tirigu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 “Simoni, Simoni, chenjera! Mulungu walola Satana kuti akupeteni nonse ngati tirigu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 “Simoni, Simoni, Satana wapempha kuti akupete ngati tirigu.

Onani mutuwo Koperani




Luka 22:31
13 Mawu Ofanana  

Tirigu wa mkate aperedwa; pakuti samampuntha osaleka; ngakhale kuyendetsapo njinga ya galeta wake, ngakhale kumphwanya ndi ziboda za akavalo ake sapera.


Pakuti taonani, ndidzalamulira, ndipo ndidzapeta nyumba ya Israele mwa amitundu onse, monga apeta tirigu m'lichero; koma silidzagwa pansi diso, ndi limodzi lonse.


Pamenepo anandionetsa Yoswa mkulu wa ansembe alikuima pamaso pa mthenga wa Yehova, ndi Satana alikuima padzanja lake lamanja, atsutsana naye.


Ndipo pamene anaimba nyimbo, anatuluka kunka kuphiri la Azitona.


Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.


Koma Ambuye anayankha nati kwa iye, Marita, Marita, uda nkhawa nuvutika ndi zinthu zambiri;


ndipo anagwa pansi, namva mau akunena naye, Saulo, Saulo, Undilondalonderanji?


kumpereka iye wochita chotere kwa Satana, kuti lionongeke thupi, kuti mzimu upulumutsidwe m'tsiku la Ambuye Yesu.


kuti asatichenjerere Satana; pakuti sitikhala osadziwa machenjerero ake.


Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:


Ndipo ndinamva mau aakulu mu Mwamba, nanena, Tsopano zafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Khristu wake; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa