Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 8:16 - Buku Lopatulika

16 Koma ayamikike Mulungu, wakupatsa khama lomweli la kwa inu mu mtima wa Tito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Koma ayamikike Mulungu, wakupatsa khama lomweli la kwa inu mu mtima wa Tito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Tiyamike Mulungu kuti adaika mumtima mwa Tito changu chomwecho chimene ife tili nacho pokuthandizani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Tithokoze Mulungu amene anayika mu mtima wa Tito changu chomwecho chimene ine ndili nacho pa inu.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 8:16
13 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene Hezekiya ndi akulu ake anadza, naona miyuluyi, analemekeza Yehova, nadalitsa anthu ake Aisraele.


Wodala Yehova Mulungu wa makolo athu, amene anaika chinthu chotere mu mtima wa mfumu, kukometsera nyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu,


Ndipo ndinauka usiku, ine ndi amuna owerengeka nane, osauza munthu yense ine choika Mulungu wanga m'mtima mwanga ndichitire Yerusalemu; panalibenso nyama ina nane, koma nyama imene ndinakhalapo.


Taonani masiku adza, ati Yehova, ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israele, ndi nyumba ya Yuda;


ndipo ndidzapangana nao pangano lamuyaya, kuti sindidzawachokera kuleka kuwachitira zabwino; koma ndidzalonga kuopsa kwanga m'mitima yao, kuti asandichokere.


Chifukwa chake ndingakhale ndalembera kwa inu, sindinachita chifukwa cha iye amene anachita choipa, kapena chifukwa cha iye amene anachitidwa choipa, koma kuti khama lanu la kwa ife lionetsedwe kwa inu pamaso pa Mulungu.


koma si ndi kufika kwake kokha, komanso ndi chitonthozo chimene anatonthozedwa nacho mwa inu, pamene anatiuza ife kukhumbitsa kwanu, kulira kwanu, changu chanu cha kwa ine; kotero kuti ndinakondwera koposa.


Nanga za Tito, ali woyanjana wanga ndi wochita nane wa kwa inu; nanga abale athu, ali atumwi a Mipingo, ali ulemerero wa Khristu.


Kotero kuti tinadandaulira Tito, kuti monga anayamba kale, chomwechonso atsirize kwa inu chisomo ichinso.


Pakuti ndilibe wina wa mtima womwewo, amene adzasamalira za kwa inu ndi mtima woona.


Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye.


Pakuti Mulungu anapatsa kumtima kwao kuchita za m'mtima mwake, ndi kuchita cha mtima umodzi ndi kupatsa ufumu wao kwa chilombo, kufikira akwaniridwa mau a Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa