Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 8:17 - Buku Lopatulika

17 Pakutitu analandira kudandaulira kwathu; koma pokhala nalo khama loposa, anatulukira kunka kwa inu mwini wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Pakutitu analandira kudandaulira kwathu; koma pokhala nalo khama loposa, anatulukira kunka kwa inu mwini wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Pakuti sadangochita zimene tidampempha, koma changu chake chinali chachikulu, kotero kuti adatsimikiza yekha zobwera kwanuko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Pakuti Tito sanangovomera kokha pempho lathu, koma yekha anafunitsitsa kwambiri kubwera kwa inu mwa iye yekha.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 8:17
5 Mawu Ofanana  

Ndinadandaulira Tito, ndipo ndinatuma mbaleyo naye. Kodi Tito anakuchenjererani kanthu? Sitinayendayende naye Mzimu yemweyo kodi? Sitinatsate mapazi omwewo kodi?


Ndipo m'menemo nditchula choyesa ine; pakuti chimene chipindulira inu, amene munayamba kale chaka chapitachi si kuchita kokha, komanso kufunira.


Kotero kuti tinadandaulira Tito, kuti monga anayamba kale, chomwechonso atsirize kwa inu chisomo ichinso.


Sindinena ichi monga kulamulira, koma kuyesa mwa khama la ena choonadi cha chikondi chanunso.


Koma ndidandaulira inu, abale, lolani mau a chidandauliro; pakutinso ndalembera inu mwachidule.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa