Ndipo pakupita paulendo pao Iye analowa m'mudzi wina; ndipo mkazi wina dzina lake Marita anamlandira Iye kunyumba kwake.
Yohane 11:5 - Buku Lopatulika Koma Yesu anakonda Marita, ndi mbale wake, ndi Lazaro. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Yesu anakonda Marita, ndi mbale wake, ndi Lazaro. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndiye kuti Yesu ankakonda Marita ndi mng'ono wake Maria ndiponso Lazaro. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anakonda Marita, mchemwali wake ndi Lazaro. |
Ndipo pakupita paulendo pao Iye analowa m'mudzi wina; ndipo mkazi wina dzina lake Marita anamlandira Iye kunyumba kwake.
Koma Marita anatekeseka ndi kutumikira kwambiri; ndipo anadzako nati, Ambuye, kodi simusamala kuti mbale wanga anandisiya nditumikire ndekha? Mumuuze tsono kuti andithandize.
Koma Ambuye anayankha nati kwa iye, Marita, Marita, uda nkhawa nuvutika ndi zinthu zambiri;
Koma panali munthu wodwala, Lazaro wa ku Betaniya, wa m'mudzi wa Maria ndi mbale wake Marita.
Chifukwa chake pamene anamva kuti anadwala, anakhala pamenepo pamalo pomwepo masiku awiri.
Ophunzira ananena ndi Iye, Rabi, Ayuda analikufuna kukuponyani miyala tsopano apa; ndipo munkanso komweko kodi?
pakuti Atate yekha akonda inu, chifukwa inu mwandikonda Ine, ndi kukhulupirira kuti Ine ndinatuluka kwa Atate.
ndipo ndinazindikiritsa iwo dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa; kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndi Ine mwa iwo.