Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 11:3 - Buku Lopatulika

3 Pamenepo alongo ake anatumiza kwa Iye, nanena, Ambuye, onani, amene mumkonda adwala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pamenepo alongo ake anatumiza kwa Iye, nanena, Ambuye, onani, amene mumkonda adwala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tsono alongo ake aja adatumiza thenga kwa Yesu kukamuuza kuti, “Ambuye, bwenzi lanu uja akudwala.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Choncho alongo ake anatumiza mawu kwa Yesu kuti, “Ambuye, uja amene Inu mumamukonda akudwala.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 11:3
16 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Tengatu mwana wako, wamwamuna wayekhayo, Isaki, amene ukondana naye, numuke ku dziko la Moriya; numpereke iye kumeneko nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri lomwe ndidzakuuza iwe.


Za oyera mtima okhala padziko lapansi, iwo ndiwo omveka mbiri, mwa iwowo muli chikondwero changa chonse.


Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire.


Koma panali munthu wodwala, Lazaro wa ku Betaniya, wa m'mudzi wa Maria ndi mbale wake Marita.


Izi anati, ndipo zitatha izi ananena nao, Lazaro bwenzi lathu ali m'tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take.


Koma ndiye Maria uja anadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira bwino, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake, amene mlongo wake Lazaro anadwala.


Ndipo Marita anati kwa Yesu, Ambuye, mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa.


Chifukwa chake Ayuda ananena, Taonani, anamkondadi!


Koma Yesu anakonda Marita, ndi mbale wake, ndi Lazaro.


Inu munditcha Ine Mphunzitsi, ndi Ambuye: ndipo munena bwino; pakuti ndine amene.


Koma mmodzi wa ophunzira ake, amene Yesu anamkonda, analikutsamira pa chifuwa cha Yesu.


Erasto anakhalira mu Korinto; koma Trofimo ndamsiya wodwala ku Mileto.


Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa