Yeremiya 4:3 - Buku Lopatulika Pakuti Yehova atero kwa anthu a Yuda ndi kwa Yerusalemu, Limani masala anu, musabzale paminga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti Yehova atero kwa anthu a Yuda ndi kwa Yerusalemu, Limani masala anu, musabzale paminga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta akuuza anthu a ku Yuda ndi anthu okhala ku Yerusalemu kuti, “Limani masala anu, musabzale pakati pa minga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zimene Yehova akunena kwa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu ndi izi: “Limani masala anu musadzale pakati pa minga. |
koma chaka chachisanu ndi chiwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo, ndipo zotsalira nyama zakuthengo zizidye; momwemo uzichita ndi munda wako wampesa, ndi munda wako wa azitona.
Mudzibzalire m'chilungamo mukolole monga mwa chifundo; limani masala anu, pakuti yafika nthawi ya kufuna Yehova, mpaka afika Iye, navumbitsira inu chilungamo.
Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mau; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma chitsamwitsa mau, ndipo akhala wopanda chipatso.
Ndipo zina zinagwa paminga, ndipo minga inakula, nkuzitsamwitsa, ndipo sizinabale zipatso.
Ndipo zija zinagwa kumingazi, ndiwo amene adamva, ndipo m'kupita kwao atsamwitsidwa ndi nkhawa, ndi chuma, ndi zokondweretsa za moyo, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu.