Ndipo Yakobo anati kwa a banja lake, ndi kwa onse amene anali ndi iye, Chotsani milungu yachilendo ili mwa inu, mudziyeretse, ndi kupindula zovala zanu:
Numeri 8:7 - Buku Lopatulika Ndipo utere nao kuwayeretsa: uwawaze madzi akuchotsa zoipa, ndipo apititse lumo pa thupi lao lonse, natsuke zovala zao, nadziyeretse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo utere nao kuwayeretsa: uwawaze madzi akuchotsa zoipa, ndipo apititse lumo pa thupi lao lonse, natsuke zovala zao, nadziyeretse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kuŵayeretsa kwake uchite motere: uŵawaze madzi oyeretsera machimo ao. Amete m'thupi monse ndi lumo, ndipo achape zovala kuti adziyeretse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Powayeretsa uchite izi: uwawaze madzi oyeretsa ndipo amete thupi lawo lonse ndi kuchapa zovala zawo kuti adziyeretse. |
Ndipo Yakobo anati kwa a banja lake, ndi kwa onse amene anali ndi iye, Chotsani milungu yachilendo ili mwa inu, mudziyeretse, ndi kupindula zovala zanu:
Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbuu woposa matalala.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka kwa anthuwo, nuwapatulitse lero ndi mawa, ndipo atsuke zovala zao.
momwemonso Iye adzawazawaza mitundu yambiri; mafumu adzamtsekera Iye pakamwa pao; pakuti chimene sichinauzidwe kwa iwo adzachiona, ndi chimene iwo sanamve adzazindikira.
Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati?
Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.
Ndipo munthu aliyense akakhudza zimenezi adzakhala wodetsedwa, natsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
Ndipo iye wakukhalira chinthu chilichonse adachikhalira wakukhayo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
Ndi iye amene anazitentha atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, ndipo atatero alowenso kuchigono.
Aliyense wakukhudza mtembo wa munthu aliyense wakufa, osadziyeretsa, aipsa chihema cha Yehova; amsadze munthuyo kwa Israele; popeza sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa; kudetsedwa kwake kukali pa iye.
Muyeretse zovala zanu zonse, zipangizo zonse zachikopa, ndi zoomba zonse za ubweya wa mbuzi, ndi zipangizo zonse za mtengo.
Ndipo Alevi anadziyeretsa, natsuka zovala zao; ndi Aroni anawapereka ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndi Aroni anawachitira chotetezera kuwayeretsa.
Popeza akhala zoikika za thupi zokha (ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe osiyanasiyana), oikidwa kufikira nthawi yakukonzanso.
Pakuti ngati mwazi wa mbuzi ndi ng'ombe zamphongo, ndi makala a ng'ombe yamthandi owazawaza pa iwo odetsedwa, upatutsa kufikira chiyeretso cha thupi;
Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m'manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.
chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Khristu;
Ndipo ndinati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwa ine, Iwo ndiwo akutuluka m'chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zao, naziyeretsa m'mwazi wa Mwanawankhosa.