Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 8:8 - Buku Lopatulika

8 Pamenepo atenge ng'ombe yamphongo ndi nsembe yake yaufa, ufa wosakaniza ndi mafuta; utengenso ng'ombe yamphongo ina ikhale nsembe yauchimo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Pamenepo atenge ng'ombe yamphongo ndi nsembe yake yaufa, ufa wosanganiza ndi mafuta; utengenso ng'ombe yamphongo ina ikhale nsembe yauchimo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Tsono iwowo atenge mwanawang'ombe wamphongo, pamodzi ndi chopereka cha chakudya wosalala wosakaniza ndi mafuta. Iweyo utenge mwanawang'ombe wina wamphongo woperekera nsembe yopepesera machimo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Atenge ngʼombe yayimuna yayingʼono ndi chopereka cha chakudya cha ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Atengenso ngʼombe ina yayimuna, yayingʼono, ya chopereka chopepesera machimo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 8:8
12 Mawu Ofanana  

Ichi ndicho uwachitire kuwapatula, andichitire ntchito ya nsembe: tenga ng'ombe yamphongo, ndi nkhosa ziwiri zamphongo zangwiro,


Ndipo uziike mu dengu limodzi, ndi kubwera nazo mudengu, pamodzi ndi ng'ombe yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo.


Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wake ukapereka nsembe yopalamula, Iye adzaona mbeu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m'manja mwake.


Chopereka chake chikakhala nsembe yopsereza ya ng'ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda chilema; abwere nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova.


Aroni azilowa pa bwalo la malo opatulika nazozo: ng'ombe yamphongo ikhale ya nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo ikhale ya nsembe yopsereza.


Ndipo munthu akabwera nacho chopereka ndicho nsembe yaufa ya kwa Yehova, chopereka chake chizikhala cha ufa wosalala; ndipo athirepo mafuta, ndi kuikapo lubani.


kukadziwika kuchimwa adachimwako, pamenepo msonkhano uzibwera nayo ng'ombe yamphongo, ikhale nsembe yauchimo, ndipo udze nayo ku khomo la chihema chokomanako.


akalakwa wansembe wodzozedwa ndi kupalamulira anthu; pamenepo azibwera nayo kwa Yehova ng'ombe yamphongo, yopanda chilema, chifukwa cha kuchimwa kwake adakuchita, ikhale nsembe yauchimo.


Tenga Aroni ndi ana ake pamodzi naye ndi zovalazo, ndi mafuta odzozawo; ndi ng'ombe ya nsembe yauchimoyo, ndi nkhosa zamphongo ziwirizo, ndi dengu la mkate wopanda chotupitsawo;


Pakuti chimene chilamulo sichinathe kuchita, popeza chinafooka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wake wa Iye yekha m'chifanizo cha thupi la uchimo, ndi chifukwa cha uchimo, natsutsa uchimo m'thupi;


Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa