Ndipo iye anati Ndileke ndimuke, chifukwa kulinkucha. Ndipo Yakobo anati, Sindidzakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa ine.
Numeri 6:27 - Buku Lopatulika Potero aike dzina langa pa ana a Israele; ndipo ndidzawadalitsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Potero aike dzina langa pa ana a Israele; ndipo ndidzawadalitsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Chauta adati, “Akamadzatchula dzina langa podalitsa Aisraele, Ine ndidzaŵadalitsadi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho akadzatchula dzina langa podalitsa Aisraeli, Ine ndidzawadalitsadi. |
Ndipo iye anati Ndileke ndimuke, chifukwa kulinkucha. Ndipo Yakobo anati, Sindidzakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa ine.
Yakobo ndipo anafunsa iye, nati, Undiuze ine dzina lako. Ndipo iye anati, Undifunsa dzina chifukwa ninji? Ndipo anamdalitsa iye pamenepo.
Ndiponso mtundu uti wa padziko lapansi ufanana ndi anthu anu, ndiwo Israele, amene Mulungu anakadziombolera akhale anthu ake, ndi kuti limveke dzina lake, ndi kukuchitirani zinthu zazikulu ndi kuchitira dziko lanu zoopsa, pamaso pa anthu anu, amene munadziombolera kuwatulutsa ku dziko la Ejipito mwa amitundu ndi milungu yao?
Ndipo Yabezi anaitana kwa Mulungu wa Israele, ndi kuti, Mundidalitse ndithu, ndi kukulitsa malire anga; ndi dzanja lanu likhale ndi ine, nimundisunge, kuti choipa chisandivute. Ndipo Mulungu anafikitsa chopempha iye.
ndipo anthu anga otchedwa dzina langa akadzichepetsa, nakapemphera, nakafuna nkhope yanga, nakatembenuka kuleka njira zao zoipa; pamenepo ndidzamvera mu Mwamba, ndi kukhululukira choipa chao, ndi kuchiritsa dziko lao.
Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo; mudzamtchinjiriza nacho chivomerezo ngati chikopa.
ndipo ndinaonekera Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, Mulungu Wamphamvuyonse; koma sindinadziwike kwa iwo ndi dzina langa YEHOVA.
yense wotchedwa dzina langa, amene ndinamlenga chifukwa cha ulemerero wanga; ndinamuumba iye; inde, ndinampanga iye.
Bwanji mukhala ngati munthu wodabwa, ngati munthu wamphamvu wosatha kupulumutsa? Koma Inu, Yehova, muli pakati pathu, titchedwa ndi dzina lanu; musatisiye.
Kapena kulankhula, osachitsimikiza? Taonani, ndalandira mau akudalitsa, popeza Iye wadalitsa, sinditha kusintha.
Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;
Ndipo anthu onse a padziko lapansi adzaona kuti akutchulani dzina la Yehova; nadzakuopani.