Numeri 4:4 - Buku Lopatulika Ntchito ya ana a Kohati m'chihema chokomanako ndi iyi, kunena za zinthu zopatulika kwambiri: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ntchito ya ana a Kohati m'chihema chokomanako ndi iyi, kunena za zinthu zopatulika kwambiri: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ntchito imene ana a Kohati ayenera kugwira m'chihema chamsonkhanomo ndi iyi: azisamala zinthu zopatulika kopambana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ntchito ya Akohati mu tenti ya msonkhano ndi iyi: kusamalira zinthu zopatulika kwambiri. |
Pamenepo Akohati anayenda, ndi kunyamula zopatulika, ndi enawo anautsiratu chihema asanafike iwowa.
Atatha Aroni ndi ana ake aamuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zake zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'chigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati m'chihema chokomanako.
koma muzitero nao kuti akhale ndi moyo, osafa ai, poyandikiza iwo zopatulika kwambirizo; Aroni ndi ana ake aamuna alowe, namuikire munthu yense ntchito yake ndi katundu wake.
kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuti agwire ntchito ya chihema chokomanako.
Uwawerenge kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuchita ntchito ya chihema chokomanako.
akati amuke a m'chigono, Aroni ndi ana ake aamuna azilowa, natsitse nsalu yotchinga, ndi kuphimba nayo likasa la mboni,
Koma sanapatse ana a Kohati kanthu; popeza ntchito yao ndiyo ya zinthu zopatulika, zimene amazisenza pa mapewa ao.
Monga ngati munthu wa paulendo, adachoka kunyumba kwake, nawapatsa akapolo ake ulamuliro, kwa munthu aliyense ntchito yake, nalamula wapakhomo adikire.