Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 4:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 “Ntchito ya Akohati mu tenti ya msonkhano ndi iyi: kusamalira zinthu zopatulika kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Ntchito ya ana a Kohati m'chihema chokomanako ndi iyi, kunena za zinthu zopatulika kwambiri:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ntchito ya ana a Kohati m'chihema chokomanako ndi iyi, kunena za zinthu zopatulika kwambiri:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ntchito imene ana a Kohati ayenera kugwira m'chihema chamsonkhanomo ndi iyi: azisamala zinthu zopatulika kopambana.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 4:4
11 Mawu Ofanana  

Davide anagawa Aleviwo mʼmagulumagulu motsatira ana a Levi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.


Kenaka Akohati ananyamuka atanyamula zinthu zopatulika. Chihema chinkayenera kuyimikidwa iwo asanafike.


“Aaroni ndi ana ake aamuna akamaliza kukutira ziwiya za ku malo wopatulika ndi zipangizo zopatulika zonse, ndipo akakonzeka kusamuka pamalopo, Akohati abwere kudzazinyamula koma asagwire zinthu zopatulikazo. Akatero adzafa. Izi ndizo zinthu zimene Akohati ayenera kunyamula mu tenti ya msonkhano.


Koma muziwachitira izi kuti asafe, akhalebe ndi moyo pamene ayandikira zinthu za ku malo wopatulika kwambiri: Aaroni ndi ana ake aamuna azipita ku malo wopatulika ndi kumamupatsa munthu aliyense ntchito yake ndi zimene ayenera kunyamula.


“Ntchito ya mafuko a Ageresoni pamene akugwira ntchito ndi kunyamula katundu ndi iyi:


Werengani amuna onse amene ali ndi zaka makumi atatu mpaka zaka makumi asanu amene amabwera kudzagwira ntchito mu tenti ya msonkhano.


Werenga amuna onse a zaka makumi atatu mpaka zaka makumi asanu zakubadwa amene akatumikire mu tenti ya msonkhano.


Pamene anthu akusamuka pa msasa, Aaroni ndi ana ake aamuna azilowa mu tenti ndi kuchotsa chinsalu chotchingira ndi kuphimba nacho bokosi la umboni.


Koma Mose sanapereke zimenezi kwa Akohati chifukwa zinthu zawo zopatulika zomwe ankayangʼanira zinali zoti azinyamula pa mapewa awo.


Zili ngati munthu amene akuchokapo. Amasiyira nyumba yake antchito ake, aliyense ndi ntchito yake; ndi kumuwuza wa pa khomo kuti azikhala maso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa