Numeri 4:3 - Buku Lopatulika3 kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuti agwire ntchito ya chihema chokomanako. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuti agwire ntchito ya chihema chokomanako. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Muŵerenge amuna kuyambira a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu, onse amene angathe kutumikira pa ntchito ya m'chihema chamsonkhano. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Werengani amuna onse amene ali ndi zaka makumi atatu mpaka zaka makumi asanu amene amabwera kudzagwira ntchito mu tenti ya msonkhano. Onani mutuwo |
Chaka chachiwiri tsono chakufika iwo kunyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, mwezi wachiwiri, Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ao otsala, ansembe ndi Alevi, ndi onse ochokera kundende kudza ku Yerusalemu, anayamba, naika Alevi a zaka makumi awiri ndi mphambu, ayang'anire ntchito ya nyumba ya Yehova.