Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 4:19 - Buku Lopatulika

koma muzitero nao kuti akhale ndi moyo, osafa ai, poyandikiza iwo zopatulika kwambirizo; Aroni ndi ana ake aamuna alowe, namuikire munthu yense ntchito yake ndi katundu wake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

koma muzitero nao kuti akhale ndi moyo, osafa ai, poyandikiza iwo zopatulika kwambirizo; Aroni ndi ana ake amuna alowe, namuikire munthu yense ntchito yake ndi katundu wake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kuti Akohatiwo asafe, akayandikira zinthu zopatulika kopambana, Aroni pamodzi ndi ana ake aloŵe, ndipo apatse aliyense mwa Akohatiwo zoti achite ndi zoti anyamule.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma muziwachitira izi kuti asafe, akhalebe ndi moyo pamene ayandikira zinthu za ku malo wopatulika kwambiri: Aaroni ndi ana ake aamuna azipita ku malo wopatulika ndi kumamupatsa munthu aliyense ntchito yake ndi zimene ayenera kunyamula.

Onani mutuwo



Numeri 4:19
6 Mawu Ofanana  

Ndipo pofika iwo ku dwale la Nakoni, Uza anatambasula dzanja lake, nachirikiza likasa la Mulungu; chifukwa ng'ombe zikadapulumuka.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tsika, chenjeza anthu, kuti angapyolere kwa Yehova kudzaona, ndipo angagwe ambiri a iwowa.


Ndipo akati amuke nacho chihemacho, Alevi amgwetse, ndipo akati achimange, Alevi achiimike; ndipo mlendo akayandikizako amuphe.


Ndipo asunge udikiro wako, ndi udikiro wa chihema chonse; koma asayandikize zipangizo za malo opatulika, ndi guwa la nsembe, kuti mungafe, iwo ndi inu.


Atatha Aroni ndi ana ake aamuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zake zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'chigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati m'chihema chokomanako.


Musamasadza fuko la mabanja a Akohati kuwachotsa pakati pa Alevi;