Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 4:19 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Koma muziwachitira izi kuti asafe, akhalebe ndi moyo pamene ayandikira zinthu za ku malo wopatulika kwambiri: Aaroni ndi ana ake aamuna azipita ku malo wopatulika ndi kumamupatsa munthu aliyense ntchito yake ndi zimene ayenera kunyamula.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

19 koma muzitero nao kuti akhale ndi moyo, osafa ai, poyandikiza iwo zopatulika kwambirizo; Aroni ndi ana ake aamuna alowe, namuikire munthu yense ntchito yake ndi katundu wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 koma muzitero nao kuti akhale ndi moyo, osafa ai, poyandikiza iwo zopatulika kwambirizo; Aroni ndi ana ake amuna alowe, namuikire munthu yense ntchito yake ndi katundu wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Kuti Akohatiwo asafe, akayandikira zinthu zopatulika kopambana, Aroni pamodzi ndi ana ake aloŵe, ndipo apatse aliyense mwa Akohatiwo zoti achite ndi zoti anyamule.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 4:19
6 Mawu Ofanana  

Atafika pa malo opunthira tirigu a Nakoni, Uza anatambalitsa dzanja lake kuti agwire Bokosi la Mulungu, chifukwa ngʼombe zinkafuna kugwa.


ndipo Yehova anati kwa iye, “Tsika ukawachenjeze anthu kuti asayesere kudutsa malire kuti adzandione chifukwa ambiri a iwo adzafa.


Pamene akusamutsa tentiyo, Alevi ndiwo aziyitsitsa, akafuna kuyimanganso, Alevi ndiwo aziyimiritsa. Wina aliyense amene adzayandikire tentiyo adzaphedwa.


Iwowo azikutumikirani ndipo azichita ntchito zonse za ku tenti, koma asamafike pafupi ndi zipangizo za ku malo opatulika kapena guwa lansembe, kuopa kuti iwo ndi inu mungafe.


“Aaroni ndi ana ake aamuna akamaliza kukutira ziwiya za ku malo wopatulika ndi zipangizo zopatulika zonse, ndipo akakonzeka kusamuka pamalopo, Akohati abwere kudzazinyamula koma asagwire zinthu zopatulikazo. Akatero adzafa. Izi ndizo zinthu zimene Akohati ayenera kunyamula mu tenti ya msonkhano.


“Onetsetsani kuti mabanja a fuko la Kohati asachotsedwe kwa Alevi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa