Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 34:4 - Buku Lopatulika

ndi malire anu adzapinda kuchokera kumwera kunka pokwera Akarabimu, ndi kupitirira ku Zini; ndi kutuluka kwake adzachokera kumwera ku Kadesi-Baranea, nadzatuluka kunka ku Hazara-Adara, ndi kupita kunka ku Azimoni;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ndi malire anu adzapinda kuchokera kumwera kunka pokwera Akarabimu, ndi kupitirira ku Zini; ndi kutuluka kwake adzachokera kumwera ku Kadesi-Baranea, nadzatuluka kunka ku Hazara-Adara, ndi kupita kunka ku Azimoni;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Malire anuwo apite kumwera, ndipo akwere phiri la Akarabimu ndi kuwolokera ku Zini. Mathero ake akhale kumwera kwa Kadesi-Baranea. Tsono apitirire mpaka ku Hazaradara, ndipo alambalale kukafika ku Azimoni.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Malirewo adzapita kummwera ndipo adzakwera phiri la Akirabimu mpaka ku Zini. Mathero ake adzakhala kummwera kwa Kadesi-Baranea. Ndipo adzapitenso ku Hazari Adari mpaka kukafika ku Azimoni,

Onani mutuwo



Numeri 34:4
9 Mawu Ofanana  

Pamenepo anakwerako, nazonda dziko kuyambira chipululu za Zini kufikira Rehobu, polowa ku Hamati.


Ndipo anamuka, nadza kwa Mose, ndi Aroni, ndi khamu lonse la ana a Israele, ku chipululu cha Parani ku Kadesi; ndipo anabwezera mau iwowa, ndi khamu lonse, nawaonetsa zipatso za dzikoli.


Ndipo ana a Israele, ndilo khamu lonse, analowa m'chipululu cha Zini mwezi woyamba; ndipo anthu anakhala mu Kadesi; kumeneko anafa Miriyamu, naikidwa komweko.


Anatero makolo anu, muja ndinawatumiza achoke ku Kadesi-Baranea kukaona dziko.


dera lanu la kumwera lidzakhala lochokera ku chipululu cha Zini, kutsata m'mphepete mwa Edomu, ndi malire anu a kumwera adzakhala ochokera ku malekezero a Nyanja ya Mchere kum'mawa;


Ndipo gawo la fuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao linafikira malire a Edomu, ku chipululu cha Zini kumwera, ku malekezero a kumwera.


Ndipo malire a Aamori anayambira pokwerera pa Akarabimu, pathanthwe ku Sela, ndi pokwererapo.