Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 15:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo gawo la fuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao linafikira malire a Edomu, ku chipululu cha Zini kumwera, ku malekezero a kumwera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo gawo la fuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao linafikira malire a Edomu, ku chipululu cha Zini kumwera, ku malekezero a kumwera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Mabanja onse a fuko la Yuda adalandira chigawo cha dzikolo motero: dziko lao lidalekeza ku malire a Edomu, mpaka ku chipululu cha Zini, kumwera kwenikweni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Chigawo cha dzikolo chimene mabanja a fuko la Yuda analandira chinafika ku malire ndi Edomu mpaka ku chipululu cha Zini kummwera kwenikweni.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 15:1
13 Mawu Ofanana  

ana aamuna a Leya: ndiwo Rubeni mwana woyamba wa Yakobo, ndi Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Zebuloni, ndi Isakara;


Ndipo nthawi yomweyo Solomoni anachita madyerero pamaso pa Yehova Mulungu wathu, ndi Israele yense pamodzi naye, msonkhano waukulu wakuyambira polowera ku Hamati kufikira ku nyanja ya ku Ejipito, masiku asanu ndi awiri, ndi masiku asanu ndi awiri ena, ndiwo masiku khumi mphambu anai.


Ndi mbali ya kumwera kuloza kumwera ndiyo kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meribati-Kadesi, ku mtsinje wa Ejipito, ndi ku Nyanja Yaikulu. Ndiyo mbali ya kumwera kuloza kumwera.


Ndi m'malire a Rubeni, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Yuda, limodzi.


Pamenepo tinafuulira kwa Yehova, ndipo anamva mau athu, natuma mthenga, natitulutsa mu Ejipito; ndipo, taonani, tili mu Kadesi, ndiwo mzinda wa malekezero a malire anu.


ndi a ku Yerusalemu, ndi a ku Idumeya, ndi a ku tsidya lina la Yordani, ndi a kufupi ku Tiro ndi Sidoni, khamu lalikulu, pakumva zazikuluzo anazichita, linadza kwa Iye.


popeza munandilakwira pakati pa ana a Israele ku madzi a Meriba wa Kadesi m'chipululu cha Zini, popeza simunandipatule Ine pakati pa ana a Israele.


Cholowa chao chinachitika ndi kulota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose, kunena za mafuko asanu ndi anai ndi fuko la hafu.


Ndi malire ao a kumwera, anayambira ku malekezero a Nyanja ya Mchere, ku nyondo yoloza kumwera;


Ndipo adzaligawa magawo asanu ndi awiri; Yuda adzakhala m'malire ake kumwera, ndi a m'nyumba ya Yosefe adzakhala m'malire mwao kumpoto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa