Numeri 3:30 - Buku Lopatulika Ndipo kalonga wa nyumba ya makolo ao ya mabanja a Akohati ndiye Elizafani mwana wa Uziyele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kalonga wa nyumba ya makolo ao ya mabanja a Akohati ndiye Elizafani mwana wa Uziyele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa pamodzi ndi Elizafani, mwana wa Uziyele, amene anali mutu wa mabanja a Akohati, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mtsogoleri wa magulu a mabanja a Kohati anali Elizafani mwana wa Uzieli. |
Ndipo Mose anaitana Misaele ndi Elizafani, ana a Uziyele, mbale wa atate wa Aroni, nanena nao, Senderani pafupi, nyamulani abale anu muwachotse pakhomo pa malo opatulika kunka nao kunja kwa chigono.
Banja la Aamuramu, ndi banja la Aizihara, ndi banja la Ahebroni, ndi banja la Auziyele ndiwo a Kohati; ndiwo mabanja a Akohati.
Ndipo udikiro wao ndiwo likasa, ndi gome, ndi choikaponyali, ndi maguwa a nsembe, ndi zipangizo za malo opatulika zimene achita nazo, ndi nsalu yotchinga, ndi ntchito zake zonse.
Atatha Aroni ndi ana ake aamuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zake zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'chigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati m'chihema chokomanako.
Ntchito ya ana a Kohati m'chihema chokomanako ndi iyi, kunena za zinthu zopatulika kwambiri: