Numeri 3:21 - Buku Lopatulika Banja la Libini, ndi mabanja a Simei, ndiwo a Geresoni; ndiwo mabanja a Geresoni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Banja la Libini, ndi mabanja a Simei, ndiwo a Geresoni; ndiwo mabanja a Geresoni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Alibini ndi Asimei anali mabanja otuluka mwa Geresoni. Ameneŵa ndiwo anali mabanja a Ageresoni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kwa Geresoni kunali banja la Alibini, banja la Asimei. Amenewa ndiwo anali mabanja a Ageresoni. |
Ndipo maina a ana aamuna a Levi, mwa kubadwa kwao ndiwo: Geresoni, ndi Kohati, ndi Merari; ndipo zaka za moyo wa Levi ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.
banja la nyumba ya Levi pa lokha, ndi akazi ao pa lokha; banja la Asimei pa okha, ndi akazi ao pa okha;
Awa ndi mabanja a Alevi: banja la Alibini, banja la Ahebroni, banja la Amali, banja la Amusi, banja la Akora. Ndipo Kohati anabala Amuramu.
Ndi ana a Merari monga mwa mabanja ao: Mali ndi Musi. Awa ndi mabanja a Alevi monga mwa nyumba za makolo ao.
Owerengedwa ao, powawerenga amuna onse, kuyambira mwana wa mwezi umodzi ndi mphambu, owerengedwa ao ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu.
Ndipo ana a Geresoni analandira molota maere motapa pa mabanja a fuko la Isakara, ndi pa fuko la Asere, ndi pa fuko la Nafutali, ndi pa hafu la fuko la Manase mu Basani, mizinda khumi ndi itatu.