Ndi ana aamuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana aamuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli.
Numeri 26:21 - Buku Lopatulika Ndipo ana a Perezi ndiwo: Hezironi, ndiye kholo la banja la Ahezironi; Hamuli, ndiye kholo la banja la Ahamuli. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ana a Perezi ndiwo: Hezironi, ndiye kholo la banja la Ahezironi; Hamuli, ndiye kholo la banja la Ahamuli. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ana aamuna a Perezi anali aŵa: Hezironi anali kholo la banja la Ahezironi. Hamuli anali kholo la banja la Ahamuli. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zidzukulu za Perezi zinali izi: kuchokera mwa Hezironi, fuko la Ahezironi; kuchokera mwa Hamuli, fuko la Ahamuli. |
Ndi ana aamuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana aamuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli.
Ndipo ana a Yuda monga mwa mabanja ao ndiwo: Sela, ndiye kholo la banja la Asela; Perezi, ndiye kholo la banja la Aperezi; Zera, ndiye kholo la banja la Azera.
Iwo ndiwo mabanja a Yuda monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi kudza mazana asanu.
Iwo ndiwo mabanja a Arubeni; owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu.
ndi Yuda anabala Perezi ndi Zera mwa Tamara; ndi Perezi anabala Hezironi; ndi Hezironi anabala Ramu;