Chomwecho Yehova anatumiza mliri pa Israele kuyambira m'mawa kufikira nthawi yoikika; ndipo anafapo anthu zikwi makumi asanu ndi awiri kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.
Numeri 25:9 - Buku Lopatulika Ndipo akufa nao mliri ndiwo zikwi makumi awiri ndi zinai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo akufa nao mliri ndiwo zikwi makumi awiri ndi zinai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe anthu okwanira 24,000 anali atafa kale ndi mliriwo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa mliriwo, anthu okwana 24,000 anafa. |
Chomwecho Yehova anatumiza mliri pa Israele kuyambira m'mawa kufikira nthawi yoikika; ndipo anafapo anthu zikwi makumi asanu ndi awiri kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.
Ndipo kunali, utatha mliriwo, Yehova ananena ndi Mose ndi Eleazara mwana wa Aroni wansembe, nati,
Taonani, awa analakwitsa ana a Israele pa Yehova ndi cha Peori chija, monga adawapangira Balamu; kotero kuti kunali mliri m'khamu la Yehova.
Kapena tisachite dama monga ena a iwo anachita dama, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi awiri ndi zitatu.