Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 25:8 - Buku Lopatulika

8 natsata munthu Mwisraele m'hema, nawapyoza onse awiri, munthu Mwisraele ndi mkaziyo m'mimba mwake. Pamenepo mliri unaletseka kwa ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 natsata munthu Mwisraele m'hema, nawamoza onse awiri, munthu Mwisraele ndi mkaziyo m'mimba mwake. Pamenepo mliri unaletseka kwa ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Ndipo adatsatira Mwisraele uja mpaka kukaloŵa m'chipinda cham'kati, nabaya onse aŵiriwo, Mwisraeleyo pamodzi ndi mkaziyo. Motero mliri udaleka pakati pa Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ndipo anatsatira Mwisraeliyu mpaka mʼtenti yake. Anasolola mkondowo ndi kubaya awiriwo kupyola Mwisraeliyo mpaka mʼthupi la mkaziyo. Pamenepo mliri unaleka pakati pa Aisraeli.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 25:8
10 Mawu Ofanana  

Naika mafupa a Saulo ndi Yonatani mwana wake ku dziko la Benjamini mu Zela, m'manda a Kisi atate wake; nachita zonse inalamulira mfumu. Ndipo pambuyo pake Mulungu anapembedzeka za dzikolo.


Ndipo Davide anamangirapo Yehova guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika. Momwemo Yehova anapembedzeka chifukwa cha dziko, ndi mliri wa pa Israele unalekeka.


Davide tsono anati kwa Orinani, Ndipatse padwale pano kuti ndimangepo guwa la nsembe la Yehova; undipatse ili pa mtengo wake wonse, kuti mliri ulekeke pa anthu.


Chipangano changa chinali naye cha moyo ndi cha mtendere; ndipo ndinampatsa izi kuti aope; nandiopa, naopsedwa chifukwa cha dzina langa.


Yense wakuyandikiza chihema cha Yehova amwalira; kodi tidzatha nkufa?


Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, wabweza kuzaza kwanga pa ana a Israele, popeza anachita nsanje ndi nsanje yanga pakati pao, kotero kuti sindinawathe ana a Israele m'nsanje yanga.


Ndipo Mose anati kwa oweruza a Israele, Iphani, yense anthu ake adaphatikanawo ndi Baala-Peori.


Ndipo anamuunjikira mulu waukulu wamiyala, wokhalako kufikira lero lino; ndipo Yehova anatembenuka kusiya mkwiyo wake waukulu. Chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo, Chigwa cha Akori, mpaka lero lino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa