Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 25:7 - Buku Lopatulika

7 Pamene Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, anachiona, anauka pakati pa khamu, natenga nthungo m'dzanja lake;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Pamene Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, anachiona, anauka pakati pa khamu, natenga nthungo m'dzanja lake;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Finehasi mwana wa Eleazara, mdzukulu wa Aroni, ataona zimenezo, adadzuka nasiya mpingowo, nakatenga mkondo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Finehasi mwana wa Eliezara, mwana wa wansembe Aaroni ataona izi, anachoka pa msonkhanowo, natenga mkondo mʼdzanja lake.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 25:7
12 Mawu Ofanana  

ndi Finehasi mwana wa Eleazara anali mtsogoleri wao kale, ndipo Yehova anali naye.


mwana wa Abisuwa mwana wa Finehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe wamkulu.


Pamenepo panauka Finehasi, nachita chilango: Ndi mliriwo unaletseka.


Ndipo ana a Levi anachita monga mwa mau a Mose; ndipo adagwa tsiku lija anthu ngati zikwi zitatu.


Ndipo Eleazara mwana wa Aroni anadzitengera mkazi wa ana aakazi a Putiyele akhale mkazi wake, ndipo anambalira Finehasi. Amenewo ndi akulu a makolo a Alevi mwa mabanja ao.


Chipangano changa chinali naye cha moyo ndi cha mtendere; ndipo ndinampatsa izi kuti aope; nandiopa, naopsedwa chifukwa cha dzina langa.


Ndipo Mose anawatuma a fuko limodzi chikwi chimodzi, kunkhondo, iwowa ndi Finehasi mwana wa Eleazara wansembe, kunkhondo, ndi zipangizo zopatulika, ndi malipenga oliza m'dzanja lake.


Ndipo ana a Israele anatumiza kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase, ku dziko la Giliyadi, Finehasi mwana wa Eleazara wansembe,


namaima ku likasalo Finehasi mwana wa Eleazara mwana wa Aroni, masiku aja; nati, Kodi nditulukenso kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga, kapena ndileke? Ndipo Yehova anati, Kwerani, pakuti mawa ndidzampereka m'dzanja lako.


Ndipo mzimu woipa wochokera kwa Yehova unali pa Saulo, pakukhala iye m'nyumba mwake, ndi mkondo wake m'dzanja lake; ndipo Davide anaimba ndi dzanja lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa