Numeri 31:16 - Buku Lopatulika16 Taonani, awa analakwitsa ana a Israele pa Yehova ndi cha Peori chija, monga adawapangira Balamu; kotero kuti kunali mliri m'khamu la Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Taonani, awa analakwitsa ana a Israele pa Yehova ndi cha Peori chija, monga adawapangira Balamu; kotero kuti kunali mliri m'khamu la Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Paja akazi ameneŵa adatsata uphungu wa Balamu, nasokeretsa Aisraele kuti asachitenso zokhulupirika pamaso pa Chauta ku Peori kuja, kotero kuti mliri udagwera mpingo wa Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Paja iwo ndi amene ankatsatira uphungu wa Balaamu ndiponso ndi amene anachititsa Aisraeli kuti asiye Yehova pa zimene zinachitika ku Peori, kotero mliri unagwera anthu a Yehova. Onani mutuwo |