M'dziko momwemo iye anatuluka kunka ku Asiriya, namanga Ninive, ndi mzinda wa Rehoboti, ndi Kala,
Numeri 24:22 - Buku Lopatulika Koma Kaini adzaonongeka, kufikira Asiriya adzakumanga nsinga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Kaini adzaonongeka, kufikira Asiriya adzakumanga nsinga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa komabe mudzaonongeka inu ana a Kaini, mudzakhala mu ukapolo wa Asuri nthaŵi yaitali.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero komabe inu Akeni mudzawonongedwa, pamene Asuri adzakutengeni ukapolo.” |
M'dziko momwemo iye anatuluka kunka ku Asiriya, namanga Ninive, ndi mzinda wa Rehoboti, ndi Kala,
anayandikira kwa Zerubabele, ndi kwa akulu a nyumba za makolo, nanena nao, Timange pamodzi nanu; pakuti timfuna Mulungu wanu monga inu, ndipo timamphera nsembe chiyambire masiku a Esarahadoni mfumu ya Asiriya, amene anatikweretsa kuno.
Asiriya sadzatipulumutsa; sitidzayenda pa akavalo, ndipo sitidzanenanso kwa ntchito ya manja athu, Inu ndinu milungu yathu; pakuti mwa Inu ana amasiye apeza chifundo.