Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 10:11 - Buku Lopatulika

11 M'dziko momwemo iye anatuluka kunka ku Asiriya, namanga Ninive, ndi mzinda wa Rehoboti, ndi Kala,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 M'dziko momwemo iye anatuluka kunka ku Asiriya, namanga Ninive, ndi mudzi wa Rehoboti, ndi Kala,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Iyeyu adachoka ku Sinara nakakhala ku Asiriya, ndipo adakamanga mizinda ya Ninive, Rehobotiiri, Kala,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Atachoka mʼdziko limeneli anapita ku Asiriya kumene anakamanga Ninive, Rehoboti-Iri, Kala,

Onani mutuwo Koperani




Genesis 10:11
17 Mawu Ofanana  

ndi Reseni pakati pa Ninive ndi Kala: umenewo ndi mzinda waukulu.


Nachoka Senakeribu mfumu ya Asiriya, namuka, nabwerera, nakhala ku Ninive.


anayandikira kwa Zerubabele, ndi kwa akulu a nyumba za makolo, nanena nao, Timange pamodzi nanu; pakuti timfuna Mulungu wanu monga inu, ndipo timamphera nsembe chiyambire masiku a Esarahadoni mfumu ya Asiriya, amene anatikweretsa kuno.


Asiriya anaphatikana nao; anakhala dzanja la ana a Loti.


Ndipo Senakeribu, mfumu ya Asiriya, anachoka, namuka, nabwerera, nakhala pa Ninive.


Harani ndi Kane ndi Edeni, amalonda a ku Sheba Asiriya ndi Kilimadi, anagulana nawe malonda.


Asiriya ali komwe ndi msonkhano wake wonse, manda ake amzinga; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga;


Asiriya sadzatipulumutsa; sitidzayenda pa akavalo, ndipo sitidzanenanso kwa ntchito ya manja athu, Inu ndinu milungu yathu; pakuti mwa Inu ana amasiye apeza chifundo.


Nyamuka, pita ku Ninive, mzinda waukuluwo, nulalikire motsutsana nao; pakuti choipa chao chandikwerera pamaso panga.


Ndipo iwo adzatha dziko la Asiriya ndi lupanga, ndi dziko la Nimirodi, ndilo polowera pake; ndipo adzatilanditsa kwa a ku Asiriya pamene alowa m'dziko lathu, pamene aponda m'kati mwa malire athu.


Katundu wa Ninive. Buku la masomphenya a Nahumu wa ku Elikosi.


Koma Ninive wakhala chiyambire chake ngati thamanda lamadzi; koma athawa. Imani, Imani! Ati, koma palibe wocheuka.


Ndipo kudzali kuti onse akupenyerera iwe adzakuthawa, nadzati, Ninive wapasuka, adzamlira maliro ndani? Ndidzakufunira kuti akukutonthoza?


Ndipo adzatambasulira dzanja lake kumpoto nadzaononga Asiriya, nadzasanduliza Ninive akhale bwinja, wouma ngati chipululu.


Koma Kaini adzaonongeka, kufikira Asiriya adzakumanga nsinga.


Koma zombo zidzafika kuchokera ku dooko la Kitimu, ndipo adzasautsa Asiriya, nadzasautsa Eberi, koma iyenso adzaonongeka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa