Anthu akutumikire iwe, mitundu ikuweramire iwe; uchite ufumu pa abale ako, ana a amai ako akuweramire iwe. Wotemberereka aliyense akutemberera iwe, wodalitsika aliyense akudalitsa iwe.
Numeri 24:18 - Buku Lopatulika Ndi Edomu adzakhala akeake, Seiri lomwe lidzakhala lakelake, ndiwo adani ake; koma Israele adzachita zamphamvu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi Edomu adzakhala akeake, Seiri lomwe lidzakhala lakelake, ndiwo adani ake; koma Israele adzachita zamphamvu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Dziko la Edomu lidzalandidwa, Seiri mdani wake adzagonjetsedwa, pamene Aisraele adzakhala akupambanabe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Edomu adzagonjetsedwa; Seiri, mdani wake, adzawonongedwa koma mphamvu za Israeli zidzachuluka. |
Anthu akutumikire iwe, mitundu ikuweramire iwe; uchite ufumu pa abale ako, ana a amai ako akuweramire iwe. Wotemberereka aliyense akutemberera iwe, wodalitsika aliyense akudalitsa iwe.
Udzakhala ndi moyo ndi lupanga lako, nudzakhala kapolo wa mphwako. Ndipo padzakhala pamene udzapulumuka, udzachotsa goli lake pakhosi pako.
Ndipo Yakobo anatumiza amithenga patsogolo pake kwa Esau mkulu wake, ku dziko la Seiri, kudera la ku Edomu.
Ndipo anaika maboma mu Edomu; m'dziko lonse la Edomu anaika maboma, ndipo Aedomu onse anasanduka anthu a Davide. Ndipo Yehova anasunga Davide kulikonse anamukako.
Ndipo Yehova anamuutsira Solomoni mdani, ndiye Hadadi Mwedomu; iyeyo anali wa mbumba ya mfumu ya ku Edomu.
Pakuti pamene Davide adali mu Edomu, ndipo Yowabu kazembe wa nkhondo adanka kukaika akufawo, atapha amuna onse mu Edomu;
Pakuti lupanga langa lakhuta kumwamba; taonani, lidzatsikira pa Edomu, ndi pa anthu amene ndawatemberera, kuti aweruzidwe.
Ndani uyu alikudza kuchokera ku Edomu, ndi zovala zonyika zochokera ku Bozira? Uyu wolemekezeka m'chovala chake, nayenda mu ukulu wa mphamvu zake? Ndine amene ndilankhula m'cholungama, wa mphamvu yakupulumutsa.
Tsiku lomwelo ndidzautsa msasa wa Davide udagwawo, ndi kukonzanso zopasuka zake; ndipo ndidzautsa zogumuka zake, ndi kuumanga monga masiku a kalelo;
kuti alandire otsala a Edomu akhale cholowa chao, ndi amitundu onse a kutchedwa dzina langa, ati Yehova wakuchita izi.
Koma Edomu ananena naye, Usapitire pakati pa ine, kuti ndingatuluke kukomana nawe ndi lupanga.