Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 9:12 - Buku Lopatulika

12 kuti alandire otsala a Edomu akhale cholowa chao, ndi amitundu onse a kutchedwa dzina langa, ati Yehova wakuchita izi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 kuti alandire otsala a Edomu akhale cholowa chao, ndi amitundu onse a kutchedwa dzina langa, ati Yehova wakuchita izi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Nthaŵi imeneyo Aisraele otsala adzagonjetsa zimene zatsala za ku Edomu, pamodzi ndi maiko onse amene amadziŵika ndi dzina langa.” Akuterotu Chauta, amene adzachitedi zimene wanenazi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 kuti adzatengenso otsala a Edomu ndi mitundu yonse imene imatchedwa ndi dzina langa,” akutero Yehova amene adzachita zinthu izi.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 9:12
17 Mawu Ofanana  

Anthu akutumikire iwe, mitundu ikuweramire iwe; uchite ufumu pa abale ako, ana a amai ako akuweramire iwe. Wotemberereka aliyense akutemberera iwe, wodalitsika aliyense akudalitsa iwe.


Ndipo anayankha Isaki nati kwa Esau, Taona, ndamuyesa iye mkulu wako, ndi abale ake onse ndampatsa iye akhale akapolo ake; ndakhazikitsa iye ndi tirigu ndi vinyo; nanga pamenepo mwana wanga, ndidzakuchitira iwe chiyani?


Mowabu ndiye mkhate wanga; pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga. Filistiya, fuulatu chifukwa cha ine.


Ndipo adzagudukira mapewa a Afilisti kumadzulo; pamodzi adzafunkha ana a kum'mawa; adzatambasula dzanja lao pa Edomu ndi pa Mowabu; ndipo ana a Amoni adzawamvera.


yense wotchedwa dzina langa, amene ndinamlenga chifukwa cha ulemerero wanga; ndinamuumba iye; inde, ndinampanga iye.


Ife takhala ngati iwo amene simunawalamulire konse, ngati iwo amene sanatchedwe dzina lanu.


Iwo amene sanafunse za Ine andifunafuna; ndi iwo amene sanandipwaire andipeza; ndinati, Taonani Ine, taonani Ine, kwa mtundu umene sunatchule dzina langa.


Bwanji mukhala ngati munthu wodabwa, ngati munthu wamphamvu wosatha kupulumutsa? Koma Inu, Yehova, muli pakati pathu, titchedwa ndi dzina lanu; musatisiye.


Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala kwa ine chikondwero ndi chisangalalo cha mtima wanga; pakuti ndatchedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu.


ndipo ndidzagulitsa ana ako aamuna ndi aakazi m'dzanja la ana a Yuda; ndipo iwo adzawagulitsa kwa anthu a Seba, kwa anthu okhala kutali; pakuti Yehova wanena.


Chinkana Edomu akuti, Taphwanyika, koma tidzabwera ndi kumanganso mabwinja; atero Yehova wa makamu, Adzamanga, koma Ine ndidzapasula; ndipo adzawatcha, Dziko la choipa, ndiponso, Anthu amene Yehova akwiya nao chikwiyire.


Kuti anthu otsalira afunefune Ambuye, ndi amitundu onse amene dzina langa linatchulidwa pa iwo,


ati Ambuye, amene azidziwitsa zinthu zonsezo chiyambire dziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa