Ndipo Davide anati kwa Natani, Ndinachimwira Yehova. Natani nati kwa Davide, Ndiponso Yehova wachotsa tchimo lanu, simudzafa.
Numeri 22:34 - Buku Lopatulika Pamenepo Balamu anati kwa mthenga wa Yehova, Ndachimwa, popeza sindinadziwe kuti munaima mondiletsa m'njira; ndipo tsopano, ngati chikuipirani, ndibwerera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Balamu anati kwa mthenga wa Yehova, Ndachimwa, popeza sindinadziwa kuti munaima mondiletsa m'njira; ndipo tsopano, ngati chikuipirani, ndibwerera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Balamu adayankha mngelo wa Chauta uja kuti, “Ndachimwa. Sindinalikudziŵa kuti mukunditsekera njira. Nchifukwa chake tsono, ngati zakuipirani, ndibwerera.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Balaamu anati kwa mngelo wa Yehova uja, “Ndachimwa. Sindinadziwe kuti munayima pa njira kunditsutsa. Tsopano ngati Inu simunakondwe, ineyo ndibwerera.” |
Ndipo Davide anati kwa Natani, Ndinachimwira Yehova. Natani nati kwa Davide, Ndiponso Yehova wachotsa tchimo lanu, simudzafa.
Ndipo Farao anatumiza, naitana Mose ndi Aroni, nanena nao, Ndachimwa tsopano; Yehova ndiye wolungama, ine ndi anthu anga ndife oipa.
Ndipo anthu anaipa, namadandaula m'makutu a Yehova; ndipo pamene Yehova anamva anapsa mtima; ndi moto wa Yehova unayaka pakati pao, nunyeketsa ku chilekezero cha chigono.
Ndipo anauka mamawa, nakwera pamwamba paphiri, nati, Tili pano, tidzakwera kunka ku malo amene Yehova ananena; popeza tachimwa.
koma bulu anandiona, nandipatukira nthawi izi zitatu pondiona; akadapanda kundipatukira, ndikadakupha iwe ndithu, ndi kumsunga iye wamoyo.
Ndipo Saulo anati kwa Samuele, Ndinachimwa; pakuti ndinalumpha lamulo la Yehova, ndi mau anu omwe; chifukwa ndinaopa anthuwo, ndi kumvera mau ao.
Pomwepo iye anati, Ndinachimwa, koma mundichitire ulemu tsopano pamaso pa akulu a anthu anga, ndi pamaso pa Israele, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova Mulungu wanu.
Nati kwa Davide, Iwe ndiwe wolungama woposa ine; popeza unandibwezera zabwino, koma ine ndinakubwezera zoipa.
Pamenepo Saulo anati, Ndinachimwa; bwera, mwana wanga Davide; pakuti sindidzakuchitiranso choipa, popeza moyo wanga unali wa mtengo wapatali pamaso pako lero; ona, ndinapusa ndi kulakwa kwakukulu.