Numeri 13:8 - Buku Lopatulika Wa fuko la Efuremu, Hoseya mwana wa Nuni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Wa fuko la Efuremu, Hoseya mwana wa Nuni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa M'fuko la Efuremu, adatuma Hoseya mwana wa Nuni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kuchokera ku fuko la Efereimu, Hoseya mwana wa Nuni; |
Ndipo pamene Yoswa anamva phokoso la kufuula kwa anthu, anati kwa Mose, Kuli phokoso la nkhondo kuchigono.
Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose kuyambira ubwana wake, anayankha nati, Mose, mfumu yanga, aletseni.
Awa ndi maina a amunawo Mose anawatumira azonde dziko. Ndipo Mose anamutcha Hoseya mwana wa Nuni Yoswa.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ayandikira masiku ako akuti uyenera kufa; kaitane Yoswa, nimuoneke m'chihema chokomanako, kuti ndimlangize. Namuka Mose ndi Yoswa, naoneka m'chihema chokomanako.
Ndipo anauza Yoswa mwana wa Nuni, nati Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao ana a Israele m'dziko limene ndinawalumbirira; ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe.
Ndipo anadza Mose nanena mau onse a nyimbo iyi m'makutu mwa anthu, iye, ndi Yoswa mwana wa Nuni.
Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anadzala ndi mzimu wanzeru; popeza Mose adamuikira manja ake; ndi ana a Israele anamvera iye, nachita monga Yehova adauza Mose.
Ndipo anamyankha Yoswa, nati, Zonse mwatilamulira tidzachita, ndipo kulikonse mutitumako tidzamuka.
monga mwa lamulo la Yehova anampatsa mzinda umene anawapempha, ndiwo Timnati-Sera, ku mapiri a Efuremu; ndipo anamanga mzindawo nakhala m'mwemo.