Pamenepo kazembe amene mfumu ankatsamira padzanja lake anamyankha munthu wa Mulungu, nati, Taonani, Yehova angachite mazenera m'mwamba chidzachitika ichi kodi? Nati iye, Taona, udzachiona ndi maso ako, koma iwe sudzadyako ai.
Numeri 11:22 - Buku Lopatulika Kodi adzawaphera magulu a nkhosa ndi ng'ombe, kuwakwanira? Kapena kodi nsomba zonse za m'nyanja zidzawasonkhanira pamodzi, kuwakwanira? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kodi adzawaphera magulu a nkhosa ndi ng'ombe, kuwakwanira? Kapena kodi nsomba zonse za m'nyanja zidzawasonkhanira pamodzi, kuwakwanira? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi zidzaphedwa nkhosa kapena ng'ombe zingati kuti ziŵakwanire? Ngakhale nsomba zonse zam'nyanja, kodi zingathe kukwanira?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi ngakhale titapha nkhosa ndi ngʼombe, zingawakwanire? Ngakhale titagwira nsomba zonse za mʼnyanja, kodi zingawakwanire iwowa?” |
Pamenepo kazembe amene mfumu ankatsamira padzanja lake anamyankha munthu wa Mulungu, nati, Taonani, Yehova angachite mazenera m'mwamba chidzachitika ichi kodi? Nati iye, Taona, udzachiona ndi maso ako, koma iwe sudzadyako ai.
Ndidzaiona kuti nyama yakuwapatsa anthu awa onse? Pakuti amalirira ine, ndi kuti, Tipatseni nyama, tidye.
Ndipo Mose anati, Anthu amene ndili pakati pao, ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda pansi, ndipo Inu mwanena, Ndidzawapatsa nyama, kuti adye mwezi wamphumphu.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Kodi dzanja la Mulungu lafupikira? Tsopano udzapenya ngati mau anga adzakuchitikira kapena iai.
Ndipo ophunzira ananena kwa Iye, Tiione kuti mikate yotere m'chipululu yakukhutitsa unyinji wotere wa anthu?
Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Apatseni kudya ndinu. Ndipo iwo ananena naye, Kodi tikapita ife ndi kugula mikate ya pa marupiya atheka mazana awiri, ndi kuwapatsa kudya?
Ndipo ophunzira ake anamyankha Iye, kuti, Munthu adzatha kutenga kuti mikate yakukhutitsa anthu awa m'chipululu muno?
Ndipo Zekariya anati kwa mngelo, Ndidzadziwitsa ichi ndi chiyani? Pakuti ndine nkhalamba, ndipo zaka zake za mkazi wanga zachuluka.
Pali mnyamata pano, amene ali nayo mikate isanu yabarele, ndi tinsomba tiwiri; koma nanga izi zikwanira bwanji ambiri otere?