Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 11:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo Mose anati, Anthu amene ndili pakati pao, ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda pansi, ndipo Inu mwanena, Ndidzawapatsa nyama, kuti adye mwezi wamphumphu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo Mose anati, Anthu amene ndili pakati pao, ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda pansi, ndipo Inu mwanena, Ndidzawapatsa nyama, kuti adye mwezi wamphumphu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Koma Mose adati, “Anthu amene ndikuyenda nawoŵa akukwanira 600,000. Ndipo Inu mwanena kuti, ‘Ndiŵapatsa nyama kuti adye mwezi wathunthu.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Koma Mose anati, “Taonani pano ndili pakati pa anthu 600,000 amene ndi kuyenda nawo ndipo Inuyo mukuti, ‘Ndidzawapatsa nyama kuti adye mwezi wathunthu!’

Onani mutuwo Koperani




Numeri 11:21
9 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;


Ndipo ana a Israele anayenda ulendo wakuchokera ku Ramsesi kufikira ku Sukoti, zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda okha, ndiwo amuna, osawerenga ana.


Munthu mmodzi anapereka beka, ndiwo limodzi la magawo awiri la sekeli, kuyesa sekeli wa malo opatulika, anatero onse akupita kunka kwa owerengedwawo, kuyambira munthu wa zaka makumi awiri ndi oposa, ndiwo anthu zikwi mazana asanu ndi limodzi kudza zitatu, ndi mazana asanu mphambu makumi asanu.


inde owerengedwa onse ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu.


Ndidzaiona kuti nyama yakuwapatsa anthu awa onse? Pakuti amalirira ine, ndi kuti, Tipatseni nyama, tidye.


koma mwezi wamphumphu, kufikira ibwera m'mphuno mwako, ndi kuti ufukidwa nayo, pakuti mwakaniza Yehova wakukhala pakati pa inu, ndi kulira pamaso pake, ndi kuti, Tinatulukiranji mu Ejipito?


Kodi adzawaphera magulu a nkhosa ndi ng'ombe, kuwakwanira? Kapena kodi nsomba zonse za m'nyanja zidzawasonkhanira pamodzi, kuwakwanira?


Amenewo ndiwo anawerengedwa a ana a Israele monga mwa nyumba za makolo ao; owerengedwa onse a m'zigono, monga mwa makamu ao, ndiwo zikwi makumi khumi kasanu ndi kamodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu.


Iwo ndiwo owerengedwa ao a ana a Israele, zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu chimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa