Numeri 11:23 - Buku Lopatulika23 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Kodi dzanja la Mulungu lafupikira? Tsopano udzapenya ngati mau anga adzakuchitikira kapena iai. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201423 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Kodi dzanja la Mulungu lafupikira? Tsopano udzapenya ngati mau anga adzakuchitikira kapena iai. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa23 Chauta adafunsanso Mose kuti, “Kodi dzanja la Chauta ndi lalifupi? Tsono uwona lero lomwe lino, ngati zichitikadi monga momwe ndanenera kapena ai.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero23 Yehova anayankha Mose kuti, “Kodi dzanja langa ndi lalifupi? Uwona tsopano ngati zimene ndanenazo zichitike kapena ayi.” Onani mutuwo |
Chifukwa chanji ndinafika osapeza munthu? Ndi kuitana koma panalibe wina woyankha? Kodi dzanja langa lafupika konse, kuti silingathe kuombola? Pena Ine kodi ndilibe mphamvu zakupulumutsa? Taona pa kudzudzula kwanga ndiumitsa nyanja, ndi kusandutsa mitsinje chipululu; nsomba zake zinunkha chifukwa mulibe madzi, ndipo zifa ndi ludzu.