Ndipo Yehova anati kwa Abramu, Tuluka iwe m'dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi kunyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe;
Numeri 10:30 - Buku Lopatulika Koma anati kwa iye, Sindidzamuka nanu; koma ndipita ku dziko langa, ndi kwa abale anga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma anati kwa iye, Sindidzamuka nanu; koma ndipita ku dziko langa, ndi kwa abale anga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma iye adayankha kuti, “Sindipita nao, ndipita kwathu kwa abale anga.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Hobabu anayankha kuti, “Ayi, sindipita nanu, ndibwerera ku dziko la kwathu ndi kwa abale anga.” |
Ndipo Yehova anati kwa Abramu, Tuluka iwe m'dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi kunyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe;
Tsono ungakhale ukadamuka chifukwa mtima wako ulinkukhumba nyumba ya atate wako, bwanji waba iwe milungu yanga?
Tamvera, mwana wamkaziwe, taona, tatchera khutu lako; uiwalenso mtundu wako ndi nyumba ya atate wako;
Nanga mutani? Munthu anali nao ana awiri; nadza iye kwa woyamba nati, Mwanawe, kagwire lero ntchito kumunda wampesa.
Munthu akadza kwa Ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sangathe kukhala wophunzira wanga.
Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.
Iwo onse adamwalira m'chikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adawaona ndi kuwalankhula kutali, navomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.
Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka kumalo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo anatuluka wosadziwa kumene akamukako.
Ndipo ana a Mkeni mlamu wake wa Mose, anakwera kutuluka m'mzinda wa m'migwalangwa pamodzi ndi ana a Yuda, nalowa m'chipululu cha Yuda chokhala kumwera kwa Aradi; namuka iwo nakhala ndi anthuwo.